Pamenepo ndinatsutsana nao aufulu a Yuda, ndinanena nao, Chinthu chanji choipa ichi muchichita, ndi kuipsa nacho tsiku la Sabata?
Mika 3:9 - Buku Lopatulika Tamvanitu ichi, akulu a nyumba ya Yakobo inu, ndi oweruza a nyumba ya Israele inu, akuipidwa nacho chiweruzo, ndi kupotoza zoongoka zonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tamvanitu ichi, akulu a nyumba ya Yakobo inu, ndi oweruza a nyumba ya Israele inu, akuipidwa nacho chiweruzo, ndi kupotoza zoongoka zonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Imvani izi inu atsogoleri a banja la Yakobe, inu olamulira a banja la Israele. Inu mumadana ndi chilungamo, mumakhotetsa zinthu zokhoza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Imvani izi, inu atsogoleri a nyumba ya Yakobo, inu olamulira nyumba ya Israeli, inu amene mumadana ndi kuweruza kolungama; ndipo mumakhotetsa zinthu zonse zolondola; |
Pamenepo ndinatsutsana nao aufulu a Yuda, ndinanena nao, Chinthu chanji choipa ichi muchichita, ndi kuipsa nacho tsiku la Sabata?
Muka, nukasonkhanitse akulu a Israele, nunene nao, Yehova, Mulungu wa makolo anu anandionekera ine, Mulungu wa Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, ndi kuti, Ndakuzondani ndithu, ndi kuona chomwe akuchitirani mu Ejipito;
Wokometsa mlandu wa wamphulupulu, ndi wotsutsa wolungama, onse awiriwa amnyansa Yehova.
Munthu woipa alandira chokometsera mlandu chotulutsa m'mfunga, kuti apatukitse mayendedwe a chiweruzo.
Kukometsa mlandu wa wamphulupulu mwatsankho sikuli kwabwino, ngakhale kuchitira chetera wolungama.
Akulu ako apanduka, ali anzao a mbala; onse akonda mitulo, natsata zokometsera milandu; iwo saweruzira amasiye; ngakhale mlandu wa mkazi wamasiye suwafika.
Anenepa, anyezimira; inde apitiriza kuchita zoipa; sanenera ana amasiye mlandu wao, kuti apindule; mlandu wa aumphawi saweruza.
Ndipo aziphunzitsa anthu anga asiyanitse pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba, ndi kuwazindikiritsa pakati pa zodetsa ndi zoyera.
Imvani ichi, ansembe inu; mverani, inu nyumba ya Israele; tcherani khutu, inu nyumba ya mfumu; pakuti chiweruzochi chinena inu; pakuti munakhala msampha ku Mizipa, ndi ukonde woyalidwa pa Tabori.
ndipo mukakaniza malemba anga, ndi moyo wanu ukanyansidwa nao maweruzo anga, kotero kuti simudzachita malamulo anga onse, koma kuthyola chipangano changa;
Mau a Yehova amene anadza kwa Mika wa ku Moreseti masiku a Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda, amene adaona za Samariya ndi Yerusalemu.
Ndipo ndinati, Imvanitu, inu akulu a Yakobo, ndi oweruza a nyumba ya Israele; simuyenera kodi kudziwa chiweruzo?
Wotembereredwa iye wakuipsa mlandu wa mlendo, mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye. Ndi anthu onse anene, Amen.