Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mika 3:8 - Buku Lopatulika

8 Koma ine ndidzala nayo mphamvu mwa Mzimu ya Yehova, ndi chiweruzo, ndi chamuna, kufotokozera Yakobo kulakwa kwake, ndi kwa Israele tchimo lake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Koma ine ndidzala nayo mphamvu mwa Mzimu ya Yehova, ndi chiweruzo, ndi chamuna, kufotokozera Yakobo kulakwa kwake, ndi kwa Israele tchimo lake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Koma ine Chauta wandidzaza ndi mphamvu, wandidzaza ndi mzimu wake. Wandidzaza ndi kulungama ndi kulimba mtima, kuti ndidzudzule a banja la Yakobe chifukwa cha zolakwa zao, kuti ndiwonetse Aisraele zoipa zao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Koma kunena za ine, ndadzazidwa ndi mphamvu, ndi Mzimu wa Yehova, ndi kulungama, ndi kulimba mtima, kuti ndilalikire za kugalukira kwa Yakobo, kwa Israeli za tchimo lake.

Onani mutuwo Koperani




Mika 3:8
28 Mawu Ofanana  

Pakuti ndadzazidwa ndi mau, ndi mzimu wa m'kati mwanga undifulumiza.


Fuula zolimba, usalekerere, kweza mau ako ngati lipenga, ndi kuwafotokozera anthu anga cholakwa chao, ndi banja la Yakobo machimo ao.


Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende;


ndikalalikire chaka chokomera Yehova, ndi tsiku lakubwezera la Mulungu wathu; ndikatonthoze mtima wa onse amene akulira maliro;


Chifukwa, taona, ndakuyesa iwe lero mzinda walinga, mzati wachitsulo, makoma amkuwa, padziko lonse, ndi pa mafumu a Yuda, ndi pa akulu ake, ndi pa ansembe ake, ndi pa anthu a m'dziko.


Ndipo ngati nditi, Sindidzamtchula Iye, sindidzanenanso m'dzina lake, pamenepo m'mtima mwanga muli ngati moto wotentha wotsekedwa m'mafupa anga, ndipo ndalema ndi kupirira, sindingathe kupiriranso.


Chifukwa chake ndadzala ndi ukali wa Yehova; ndalema ndi kudzikaniza; tsanulirani pa ana a pabwalo, ndi pa misonkhano ya anyamata, pakuti ngakhale mwamuna ndi mkazi wake adzatengedwa, okalamba ndi iye amene achuluka masiku ake.


Aneneri ako anakuonera masomphenya achabe ndi opusa; osawulula mphulupulu yako kuti abweze undende wako, koma anakuonera manenero achabe ndi opambutsa.


Wobadwa ndi munthu iwe, Dziwitsa Yerusalemu zonyansa zake, nuziti,


Udzawaweruza kodi, wobadwa ndi munthu iwe? Udzawaweruza? Uwadziwitse zonyansa za makolo ao,


Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, udzaweruza, udzauweruza mzindawo wa mwazi kodi? Uudziwitse tsono zonyansa zake zonse.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, kodi udzaweruza Ohola ndi Oholiba? Uwafotokozere tsono zonyansa zao.


M'mwemo mzimu unandinyamula ndi kuchoka nane; ndipo ndinamuka wowawidwa, womyuka mtima; koma dzanja la Yehova linandigwirizitsa.


Wobadwa ndi munthu iwe, onetsa nyumba ya Israele Kachisiyu, kuti achite manyazi ndi mphulupulu zao; ndipo ayese muyeso wake.


pakuti anawaphunzitsa monga mwini mphamvu, wosanga alembi ao.


ndi Yakobo mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake wa Yakobo, iwo anawatcha Boaneje, ndiko kuti, Ana a bingu;


Ndipo mau anga ndi kulalikira kwanga sanakhale ndi mau okopa a nzeru, koma m'chionetso cha Mzimu ndi cha mphamvu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa