Ndipo Ahitofele, pakuona kuti sautsata uphungu wake anamanga bulu wake, nanyamuka, nanka kumzinda kwao, nakonza za pa banja lake, nadzipachika, nafa, naikidwa m'manda a atate wake.
Mateyu 27:5 - Buku Lopatulika Ndipo iye anataya pansi ndalamazo pa Kachisi, nachokapo, nadzipachika yekha pakhosi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iye anataya pansi ndalamazo pa Kachisi, nachokapo, nadzipachika yekha pakhosi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yudasi adakaziponya ndalamazo m'Nyumba ya Mulungu nachokapo, kenaka nkukadzikhweza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo Yudasi anaponya ndalamazo mʼNyumba ya Mulungu nachoka. Kenaka anapita nakadzimangirira. |
Ndipo Ahitofele, pakuona kuti sautsata uphungu wake anamanga bulu wake, nanyamuka, nanka kumzinda kwao, nakonza za pa banja lake, nadzipachika, nafa, naikidwa m'manda a atate wake.
Kunali tsono, pakuona Zimiri kuti nkhondo yalowa m'mzinda, anakwera pa nsanja ya nyumba ya mfumu, nadzitenthera ndi moto nyumba ya mfumu, nafa;
Pamenepo mkazi wake ananena naye, Kodi uumiriranso kukhala wangwiro? Chitira Mulungu mwano, ufe.
Koma Inu, Mulungu, mudzawatsitsira kudzenje la chionongeko. Anthu okhetsa mwazi ndi achinyengo masiku ao sadzafikira nusu; koma ine ndidzakhulupirira Inu.
nati, Uyu ananena kuti, Ndikhoza kupasula Kachisi wa Mulunguyu, ndi kummanganso masiku atatu.
Ndipo ansembe aakulu anatenga ndalamazo, nati, Sikuloledwa kuziika m'chosonkhera ndalama za Mulungu, chifukwa ndizo mtengo wa mwazi.
monga mwa machitidwe a kupereka nsembe, adamgwera maere akufukiza zonunkhira polowa iye mu Kachisi wa Ambuye.
Pamenepo anaitana msanga mnyamata wake wosenza zida zake, nanena naye, Solola lupanga lako nundiphe, angamanenere anthu, ndi kuti, Anamupha ndi mkazi. Nampyoza mnyamata wake, nafa iye.