Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 1:9 - Buku Lopatulika

9 monga mwa machitidwe a kupereka nsembe, adamgwera maere akufukiza zonunkhira polowa iye mu Kachisi wa Ambuye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 monga mwa machitidwe a kupereka nsembe, adamgwera maere akufukiza zonunkhira polowa iye m'Kachisi wa Ambuye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Potsata dongosolo lao la ansembe, iye adaasankhidwa mwamaere kuti akaloŵe m'Nyumba ya Mulungu kukafukiza lubani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Zakariyayo anasankhidwa mwa maere, monga mwa mwambo wa unsembe, kupita mʼNyumba ya Ambuye kukafukiza lubani.

Onani mutuwo Koperani




Luka 1:9
10 Mawu Ofanana  

Ana a Amuramu: Aroni, ndi Mose; ndipo Aroni anasankhidwa kuti apatule zopatulika kwambiri, iye ndi ana ake, kosalekeza, kufukiza pamaso pa Yehova, kumtumikira, ndi kudalitsa m'dzina lake kosatha.


Koma Aroni ndi ana ake ankafukiza paguwa la nsembe yopsereza, ndi paguwa la nsembe yofukiza, chifukwa cha ntchito yonse ya malo opatulika kwambiri, ndi kuchitira Israele chowatetezera, monga mwa zonse Mose mtumiki wa Mulungu adawauza.


Koma atakhala wamphamvu, mtima wake unakwezeka momuononga, nalakwira Yehova Mulungu wake; popeza analowa mu Kachisi wa Yehova kufukiza paguwa la nsembe la chofukiza.


Ana anga, musazengereza tsopano; popeza Yehova anakusankhani inu muime pamaso pake, kumtumikira Iye, ndi kuti mukhale atumiki ake ndi kufukiza zonunkhira.


chikhale chikumbutso kwa ana a Israele, kuti mlendo, wosati wa mbeu ya Aroni, asasendere kuchita chofukiza pamaso pa Yehova; angakhale monga Kora ndi khamu lake; monga Yehova adanena naye ndi dzanja la Mose.


Ndipo iye anataya pansi ndalamazo pa Kachisi, nachokapo, nadzipachika yekha pakhosi.


Ndipo izi zitakonzeka kotero, ansembe amalowa m'chihema choyamba kosalekeza, ndi kutsiriza kulambirako;


Kodi sindinasankhule iye pakati pa mafuko onse a Israele, akhale wansembe wanga, kuti apereke nsembe paguwa langa, nafukize zonunkhira, navale efodi pamaso panga? Kodi sindinapatse banja la kholo lako zopereka zonse za kumoto za ana a Israele?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa