2 Samueli 17:23 - Buku Lopatulika23 Ndipo Ahitofele, pakuona kuti sautsata uphungu wake anamanga bulu wake, nanyamuka, nanka kumzinda kwao, nakonza za pa banja lake, nadzipachika, nafa, naikidwa m'manda a atate wake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201423 Ndipo Ahitofele, pakuona kuti sautsata uphungu wake anamanga bulu wake, nanyamuka, nanka kumudzi kwao, nakonza za pa banja lake, nadzipachika, nafa, naikidwa m'manda a atate wake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa23 Ahitofele ataona kuti anthu sadatsate malangizo ake aja, adakwera bulu wake, napita kwao ku mzinda wake. Tsono adakonza zonse za m'nyumba mwake, nadzikhweza. Motero adafa, ndipo adaikidwa m'manda a bambo wake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero23 Ahitofele ataona kuti malangizo ake sanatsatidwe, iye anakwera bulu wake napita ku mzinda wa kwawo ku nyumba yake. Iye anakonza mʼnyumba mwakemo ndi kudzimangirira. Kotero anafa nayikidwa mʼmanda a abambo ake. Onani mutuwo |