Koma iye anati, Aulesi inu, aulesi: chifukwa chake mulikunena, Timuke, timphere nsembe Yehova.
Mateyu 26:8 - Buku Lopatulika Koma m'mene ophunzira anaona, anada mtima, nanena, Chifukwa ninji kuononga kumeneku? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma m'mene ophunzira anaona, anada mtima, nanena, Chifukwa ninji kuononga kumeneku? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma pamene ophunzira ake adaona zimenezi, adaipidwa nazo nkumauzana kuti, “Chifukwa chiyani kusakaza zinthu chotere? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ophunzira ataona izi anayipidwa nafunsa kuti, “Chifukwa chiyani akuwononga chotere? |
Koma iye anati, Aulesi inu, aulesi: chifukwa chake mulikunena, Timuke, timphere nsembe Yehova.
Ndiponso ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zompindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.
Mwezi wokhala upita liti, kuti tigulitse dzinthu? Ndi Sabata, kuti titsegulire tirigu? Ndi kuchepsa efa, ndi kukulitsa sekeli, ndi kuchenjerera nayo miyeso yonyenga;
Mukutinso, Taonani, ncholemetsa ichi! Ndipo mwachipeputsa, ati Yehova wa makamu; ndipo mwabwera nazo zofunkha, ndi zotsimphina, ndi zodwala; momwemo mubwera nayo nsembe; kodi ndiyenera kuilandira kudzanja lanu? Ati Yehova.
anadza kwa Iye mkazi, anali nayo nsupa ya alabastero ndi mafuta onunkhira bwino a mtengo wapatali, nawatsanulira pamutu pake, m'mene Iye analikukhala pachakudya.
Koma anakhalako ena anavutika mtima mwa iwo okha, ndi kuti, Mafutawo atayidwa chifukwa ninji?