Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 20:24 - Buku Lopatulika

24 Ndipo m'mene khumiwo anamva, anapsa mtima ndi abale awiriwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Ndipo m'mene khumiwo anamva, anapsa mtima ndi abale awiriwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Pamene khumi ena aja adamva zimenezi, adapsera mtima abale aŵiri aja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Ophunzira khumi aja, anawapsera mtima abale awiriwo.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 20:24
13 Mawu Ofanana  

Kudzikuza kupikisanitsa; koma omwe anauzidwa uphungu ali ndi nzeru.


Iye ananena kwa iwo, Chikho changa mudzamweradi; koma kukhala kudzanja lamanja kwanga ndi kulamanzere, sikuli kwanga kupatsa, koma kuli kwa iwo omwe kwakonzedweratu ndi Atate wanga.


Koma Yesu anawaitana, nati, Mudziwa kuti mafumu a anthu amadziyesa okha ambuye ao, ndipo akulu ao amachita ufumu pa iwo.


Koma pamene Yesu anaona anakwiya, ndipo anati kwa iwo, Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse: pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa totere.


Ndipo pamene khumiwo anamva, anayamba kupsa mtima chifukwa cha Yakobo ndi Yohane.


Ndipo mkulu wa sunagoge anavutika mtima, chifukwa Yesu anachiritsa tsiku la Sabata, nayankha, nanena kwa khamulo, Alipo masiku asanu ndi limodzi, m'menemo anthu ayenera kugwira ntchito, chifukwa chake idzani kudzachiritsidwa momwemo, koma tsiku la Sabata ai.


Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziwa kudzitamanda, sichidzikuza,


musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini;


Koma mukakhala nako kaduka kowawa, ndi chotetana m'mtima mwanu, musadzitamandira, ndipo musamanama potsutsana nacho choonadi.


Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa