Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Malaki 1:13 - Buku Lopatulika

13 Mukutinso, Taonani, ncholemetsa ichi! Ndipo mwachipeputsa, ati Yehova wa makamu; ndipo mwabwera nazo zofunkha, ndi zotsimphina, ndi zodwala; momwemo mubwera nayo nsembe; kodi ndiyenera kuilandira kudzanja lanu? Ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Mukutinso, Taonani, ncholemetsa ichi! Ndipo mwachipeputsa, ati Yehova wa makamu; ndipo mwabwera nazo zofunkha, ndi zotsimphina, ndi zodwala; momwemo mubwera nayo nsembe; kodi ndiyenera kuilandira kudzanja lanu? Ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Chauta Wamphamvuzonse akunenanso kuti, “Inu mumati, ‘Ha, kutopetsa zimenezi!’ Kenakanso nkumandinyodola. Mumabwera ndi nyama zakuba kapena zopunduka kapena zodwala ngati nsembe zanu, kodi Ine ndidzazilandira?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Ndipo inu mumati, ‘Ndi zotopetsa zimenezi!’ Ndipo mumandinyogodola Ine,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Pamene inu mubweretsa nyama zakuba, zolumala kapena zodwala ndi kupereka nsembe, kodi Ine ndizilandire kuchokera mʼmanja mwanu?” Akutero Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Malaki 1:13
28 Mawu Ofanana  

Koma mfumu inati kwa Arauna, Iai; koma ndidzaligula kwa iwe pa mtengo wake, pakuti sindidzapereka kwa Yehova Mulungu wanga nsembe zopsereza zopanda mtengo wake. Momwemo Davide anagula dwalelo ndi ng'ombezo naperekapo masekeli makumi asanu a siliva.


Pakudzaonekera inu pamaso pa Ine, ndani wafuna chimenechi m'dzanja lanu, kupondaponda m'mabwalo mwanga?


Pakuti pa miyala yosalala ya m'chigwa pali gawo lako; iyo ndiyo gawo lako; ndiyo imene unaitsanulirira nsembe yothira, ndi kupereka nsembe yaufa. Kodi ndidzapembedzedwa pa zinthu zimenezi?


Pakuti Ine Yehova ndikonda chiweruziro, ndida chifwamba ndi choipa; ndipo ndidzawapatsa mphotho yao m'zoonadi; ndipo ndidzapangana nao pangano losatha.


Pamenepo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! Taonani, moyo wanga sunadetsedwe, pakuti chiyambire ubwana wanga mpaka tsopano sindinadye chinthu chakufa chokha, kapena chogwidwa ndi chilombo; simunalowanso m'kamwa mwanga nyama yonyansa.


Ansembe asadyeko kanthu kakufa kokha, kapena kogwidwa ndi chilombo, ngakhale mbalame, kapena nyama.


Israele, chikuononga ndi ichi, chakuti utsutsana ndi Ine, chithandizo chako.


Asamadya zakufa zokha, kapena zojiwa, kudzidetsa nazo; Ine ndine Yehova.


pamenepo padzali kuti popeza anachimwa, napalamula, azibweza zofunkha zimene analanda mwachifwamba, kapena chinthuchi adachiona ndi kusautsa mnzake, kapena choikiza anamuikiza, kapena chinthu chotayika anachipeza;


Mwezi wokhala upita liti, kuti tigulitse dzinthu? Ndi Sabata, kuti titsegulire tirigu? Ndi kuchepsa efa, ndi kukulitsa sekeli, ndi kuchenjerera nayo miyeso yonyenga;


Anthu anga inu, ndakuchitirani chiyani? Ndakulemetsani ndi chiyani? Chitani umboni wonditsutsa.


Mwenzi atakhala wina mwa inu wakutseka pamakomo, kuti musasonkhe moto chabe paguwa langa la nsembe! Sindikondwera nanu, ati Yehova wa makamu, ndipo sindidzalandira chopereka m'dzanja lanu.


Yehova adzalikha munthu wakuchita ichi, wogalamutsa ndi wovomereza m'mahema a Yakobo, ndi iye wopereka chopereka kwa Yehova wa makamu.


Ndi ichi mubwereza kuchichita: mukuta guwa la nsembe la Yehova ndi misozi, ndi kulira, ndi kuusa moyo; momwemo Iye sasamaliranso chopereka, kapena kulandira mokondwera m'dzanja lanu.


Ndipo pamene ponse musala kudya, musakhale ndi nkhope yachisoni, ngati onyengawo; pakuti aipitsa nkhope zao, kuti aonekere kwa anthu kuti alinkusala kudya. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.


Ndipo pamene mupemphera, musakhale monga onyengawo; chifukwa iwo akonda kuimirira ndi kupemphera m'masunagoge, ndi pa mphambano za makwalala, kuti aonekere kwa anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.


Koma ikakhala nacho chilema, yotsimphina, kapena yakhungu, chilema chilichonse choipa, musamaiphera nsembe Yehova Mulungu wanu.


Nanga umaponderezeranji nsembe yanga ndi chopereka changa, zimene ndinalamulira m'mokhalamo mwanga; ndipo uchitira ana ako ulemu koposa Ine, kudzinenepetsa inu nokha ndi zokometsetsa za zopereka zao zonse za Aisraele, anthu anga?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa