Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 26:7 - Buku Lopatulika

7 anadza kwa Iye mkazi, anali nayo nsupa ya alabastero ndi mafuta onunkhira bwino a mtengo wapatali, nawatsanulira pamutu pake, m'mene Iye analikukhala pachakudya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 anadza kwa Iye mkazi, anali nayo nsupa ya alabastero ndi mafuta onunkhira bwino a mtengo wapatali, nawatsanulira pamutu pake, m'mene Iye analikukhala pachakudya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Pamene ankadya, kudafika mai wina atatenga nsupa yagalasi ya mafuta onunkhira amtengowapatali. Adayamba kuthira mafutawo pamutu pa Yesu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 mayi wina anabwera kwa Iye ndi botolo la mafuta onunkhira a mtengowapatali, amene anathira pa mutu pake Iye akudya pa tebulo.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 26:7
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Elisa mneneriyo anaitana mmodzi wa ana a aneneri, nanena naye, Udzimangire m'chuuno, nutenge nsupa iyi ya mafuta m'dzanja mwako, numuke ku Ramoti Giliyadi.


Ndiko ngati mafuta a mtengo wake pamutu, akutsikira kundevu, inde kundevu za Aroni; akutsikira kumkawo wa zovala zake.


Ntchentche zakufa zinunkhitsa moipa ndipo zioletsa mafuta onunkhira a sing'anga; chomwecho kupusa kwapang'ono kuipitsa iye amene atchuka chifukwa cha nzeru ndi ulemu.


Zovala zako zikhale zoyera masiku onse; mutu wako usasowe mafuta.


Mafuta ako anunkhira bwino; dzina lako likunga mafuta onunkhira otsanulidwa; chifukwa chake anamwali akukonda.


Ndipo unanka kwa mfumu, utadzola mafuta ndi kuchulukitsa zonunkhira zako; ndipo unatumiza atumwi ako kutali; ndipo wadzichepetsa wekha kufikira kunsi kumanda.


Koma m'mene ophunzira anaona, anada mtima, nanena, Chifukwa ninji kuononga kumeneku?


Ndipo pakukhala Iye ku Betaniya m'nyumba ya Simoni wakhate, m'mene anaseama kudya, anadzapo mkazi ali nayo nsupa ya alabastero ya mafuta onunkhira bwino a narido weniweni a mtengo wapatali; naswa nsupayo, nawatsanulira pamutu pake.


Sunandidzoza mutu wanga ndi mafuta; koma uyu anadzoza mapazi anga ndi mafuta onunkhira bwino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa