Mateyu 14:1 - Buku Lopatulika Nthawi imeneyo Herode mfumu anamva mbiri ya Yesu, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nthawi imeneyo Herode mfumu anamva mbiri ya Yesu, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa nthaŵi imeneyo Herode, mfumu ya ku Galileya, adaamva zimene anthu ankanena za Yesu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa nthawi imeneyo Mfumu Herode anamva za mbiri ya Yesu. |
Ndipo Iye anawalamula, nanena, Yang'anirani, penyani kuti mupewe chotupitsa mkate cha Afarisi, ndi chotupitsa mkate cha Herode.
inde, ngakhale Herode yemwe; pakuti iye anambwezera Iye kwa ife; ndipo taonani, sanachite Iye kanthu kakuyenera kufa.
Ndipo pa chaka chakhumi ndi chisanu cha ufumu wa Tiberio Kaisara, pokhala Pontio Pilato kazembe wa Yudeya, ndi Herode chiwanga cha Galileya, ndi Filipo mbale wake chiwanga cha dziko la Itureya ndi la Trakoniti, ndi Lisaniasi chiwanga cha Abilene;
Koma Herode mfumu ija, m'mene Yohane anamdzudzula chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa mbale wake, ndi cha zinthu zonse zoipa Herode anazichita,
ndi Yohana, mkazi wake wa Kuza kapitao wa Herode, ndi Suzana, ndi ena ambiri, amene anawatumikira ndi chuma chao.
Ndipo kunali aneneri ndi aphunzitsi ku Antiokeya mu Mpingo wa komweko, ndiwo Barnabasi, ndi Simeoni, wonenedwa Wakuda, ndi Lusio wa ku Kirene, Manaene woleredwa pamodzi ndi Herode chiwangacho, ndi Saulo.
Pakuti zoonadi anasonkhanidwa m'mzinda muno Herode, ndi Pontio Pilato yemwe pamodzi ndi amitundu ndi anthu a Israele kumchitira choipa Mwana wanu wopatulika Yesu amene munamdzoza;