Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 4:27 - Buku Lopatulika

27 Pakuti zoonadi anasonkhanidwa m'mzinda muno Herode, ndi Pontio Pilato yemwe pamodzi ndi amitundu ndi anthu a Israele kumchitira choipa Mwana wanu wopatulika Yesu amene munamdzoza;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Pakuti zoonadi anasonkhanidwa m'mudzi muno Herode, ndi Pontio Pilato yemwe pamodzi ndi amitundu ndi anthu a Israele kumchitira choipa Mwana wanu wopatulika Yesu amene munamdzoza;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 “Zoonadi, Herode ndi Ponsio Pilato adasonkhana mumzinda muno pamodzi ndi anthu akunja, ndiponso ndi anthu a Israele, kuti alimbane ndi Yesu, Mtumiki wanu wopatulika amene mudamdzoza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Zoonadi, Herode ndi Pontiyo Pilato anasonkhana pamodzi ndi amitundu ndiponso Aisraeli, mu mzinda muno, kupanga zolimbana ndi mtumiki wanu woyera Yesu, amene Inu munamudzoza.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 4:27
53 Mawu Ofanana  

Adzatulutsa choyera m'chinthu chodetsa ndani? Nnena mmodzi yense.


Munthu nchiyani kuti akhale woyera, wobadwa ndi mkazi kuti akhale wolungama?


Potero munthu akhala bwanji wolungama kwa Mulungu? Kapena wobadwa ndi mkazi akhala woyera bwanji?


Adzikhazikitsa mafumu a dziko lapansi, nachita upo akulu pamodzi, Kutsutsana naye Yehova, ndi Wodzozedwa wake, ndi kuti,


Koma Ine ndadzoza mfumu yanga Pa Ziyoni, phiri langa loyera.


Mukonda chilungamo, ndipo mudana nacho choipa, chifukwa chake Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wadzoza inu ndi mafuta a chikondwerero koposa anzanu.


Kodi iwe sunamve, kuti ndinachita ichi kale, ndi kuchikonza nthawi zakale? Tsopano Ine ndachikwaniritsa, kuti iwe ukapasule mizinda yamalinga, isanduke miunda.


Atero Yehova, Mombolo wa Israele, ndi Woyera wake, kwa Iye amene anthu amnyoza, kwa Iye amene mtundu wathu unyasidwa naye, kwa mtumiki wa olamulira: Mafumu adzaona, nadzauka; akalonga nadzalambira chifukwa cha Yehova, amene ali wokhulupirika, ngakhale Woyera wa Israele, amene anakusankha Iwe.


Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu wombisira anthu nkhope zao; ndipo ife sitinamlemekeze.


Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende;


Nthawi imeneyo Herode mfumu anamva mbiri ya Yesu,


Pakuti Herode adamgwira Yohane, nammanga, namuika m'nyumba yandende chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa mbale wake Filipo.


Koma pakufika tsiku la kubadwa kwake kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodiasi anavina pakati pao, namkondweretsa Herode.


Nanga mutani? Munthu anali nao ana awiri; nadza iye kwa woyamba nati, Mwanawe, kagwire lero ntchito kumunda wampesa.


Ha, Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo otumidwa kwa iwe! Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m'mapiko ake, koma inu simunafune ai!


ndipo anammanga Iye, namuka naye, nampereka Iye kwa Pilato kazembeyo.


nati, Taonani, tikwera ku Yerusalemu; ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi; ndipo iwo adzamweruza kuti ayenera imfa, nadzampereka Iye kwa anthu a mitundu;


Moteronso ansembe aakulu anamtonza mwa iwo okha pamodzi ndi alembi, nanena, Anapulumutsa ena; sangathe kudzipulumutsa yekha.


Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe: chifukwa chakenso Choyeracho chikadzabadwa, chidzatchedwa Mwana wa Mulungu.


Ndipo amuna amene analikusunga Yesu anamnyoza Iye, nampanda.


Ndipo khamu lonselo linanyamuka kupita naye kwa Pilato.


Mzimu wa Ambuye uli pa Ine, chifukwa chake Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino: anandituma Ine kulalikira am'nsinga mamasulidwe, ndi akhungu kuti apenyanso, kutulutsa ndi ufulu ophwanyika,


nati, Kuyenera kuti Mwana wa Munthu amve zowawa zambiri, ndi kukanidwa ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi, ndi kuphedwa, ndi kuuka tsiku lachitatu.


Anadza kwa zake za Iye yekha, ndipo ake a mwini yekha sanamlandire Iye.


kodi inu munena za Iye, amene Atate anampatula namtuma kudziko lapansi, Uchita mwano; chifukwa ndinati, Ndili Mwana wa Mulungu?


Pamenepo anamtenga Yesu kuchokera kwa Kayafa kupita ku Pretorio; koma munali mamawa; ndipo iwo sanalowe ku Pretorio, kuti angadetsedwe, koma kuti akadye Paska.


Chifukwa chake Pilato anatulukira kunja kwa iwo, nati, Chifukwa chanji mwadza nacho cha munthu uyu?


koma mmodzi wa asilikali anamgwaza ndi nthungo m'nthiti yake, ndipo panatuluka pomwepo mwazi ndi madzi.


za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye.


Pakuti simudzasiya moyo wanga ku dziko la akufa, kapena simudzapereka Woyera wanu aone chivunde,


m'mene mutambasula dzanja lanu kukachiritsa; ndi kuti zizindikiro ndi zozizwa zichitidwe mwa dzina la Mwana wanu wopatulika Yesu.


Pakuti mkulu wa ansembe wotere anatiyenera ife, woyera mtima, wopanda choipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ochimwa, wakukhala wopitirira miyamba;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa