Mateyu 12:3 - Buku Lopatulika Koma Iye anati kwa iwo, Kodi simunawerenge chimene anachichita Davide, pamene anali ndi njala, ndi iwo amene anali naye? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Iye anati kwa iwo, Kodi simunawerenga chimene anachichita Davide, pamene anali ndi njala, ndi iwo amene anali naye? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iye adati, “Kani simudaŵerenge zimene adaachita Davide, pamene iye ndi anzake adaazingwa nayo njala? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anayankha kuti, “Kodi simunawerenge zimene anachita Davide pamene iye ndi anzake anamva njala? |
Koma Afarisi, pakuona, anati kwa Iye, Tapenyani, ophunzira anu achita chosaloleka tsiku la Sabata.
Kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, nadya mikate yoonetsa, imene yosaloleka kudya iye kapena amene anali naye, koma ansembe okhaokha.
Kapena simunawerenge kodi m'chilamulo, kuti tsiku la Sabata ansembe mu Kachisi amaipitsa tsiku la Sabata, nakhala opanda tchimo?
Ndipo Iye anayankha, nati, Kodi simunawerenga kuti Iye amene adalenga anthu pachiyambi, anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi,
nanena kwa Iye, Mulinkumva kodi chimene alikunena awa? Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Inde: simunawerenge kodi, M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza?
Koma za kuuka kwa akufa, simunawerenge kodi chomwe chinanenedwa kwa inu ndi Mulungu, kuti,
Kodi simunawerenge ngakhale lembo ili, Mwala umene anaukana omanga nyumba, womwewu unayesedwa mutu wa pangodya:
simunawerenga m'buku la Mose kodi, za chitsambacho, kuti Mulungu anati kwa iye, nanena, Ine Ndine Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo?
Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Kodi simunawerenganso ngakhale chimene anachita Davide, pamene paja anamva njala, iye ndi iwo anali naye pamodzi;