Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 12:10 - Buku Lopatulika

10 Kodi simunawerenge ngakhale lembo ili, Mwala umene anaukana omanga nyumba, womwewu unayesedwa mutu wa pangodya:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Kodi simunawerenga ngakhale lembo ili, Mwala umene anaukana omanga nyumba, womwewu unayesedwa mutu wa pangodya:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Nanga monga simudaŵerenge Malembo aja akuti, “ ‘Mwala umene amisiri omanga nyumba adaaukana, womwewo wasanduka mwala wapangondya, wofunika koposa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Kodi simunawerenge lemba lakuti: “ ‘Mwala umene amisiri omanga nyumba anawukana wakhala mwala wa pa ngodya.

Onani mutuwo Koperani




Marko 12:10
17 Mawu Ofanana  

chifukwa chake Ambuye Yehova atero, Taonani, ndiika mu Ziyoni mwala wa maziko, mwala woyesedwa mwala wa pangodya, wa mtengo wake wokhazikika ndithu; wokhulupirira sadzafulumira.


Koma Iye anati kwa iwo, Kodi simunawerenge chimene anachichita Davide, pamene anali ndi njala, ndi iwo amene anali naye?


Ndipo Iye anayankha, nati, Kodi simunawerenga kuti Iye amene adalenga anthu pachiyambi, anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi,


nanena kwa Iye, Mulinkumva kodi chimene alikunena awa? Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Inde: simunawerenge kodi, M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza?


Yesu ananena kwa iwo, Kodi simunawerenge konse m'malembo, Mwala umene anaukana omanga nyumba womwewu unakhala mutu wa pangodya: Ichi chinachokera kwa Ambuye, ndipo chili chozizwitsa m'maso mwathu?


Koma za kuuka kwa akufa, simunawerenge kodi chomwe chinanenedwa kwa inu ndi Mulungu, kuti,


simunawerenga m'buku la Mose kodi, za chitsambacho, kuti Mulungu anati kwa iye, nanena, Ine Ndine Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo?


Pamenepo mwini munda adzachita chiyani? Adzafika, nadzaononga olimawo, nadzapereka mundawo kwa ena.


Ndipo pamene mukaona chonyansa cha kupululutsa chilikuima pomwe sichiyenera (wakuwerenga azindikire), pamenepo a mu Yudeya athawire kumapiri:


Ndipo ananena nao, Simunawerenge konse chimene anachichita Davide, pamene adasowa, namva njala, iye ndi iwo amene anali pamodzi naye?


Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Kodi simunawerenganso ngakhale chimene anachita Davide, pamene paja anamva njala, iye ndi iwo anali naye pamodzi;


monganso kwalembedwa, kuti, Onani, ndikhazika mu Ziyoni mwala wakukhumudwa nao, ndi thanthwe lophunthwitsa; ndipo wakukhulupirira Iye sadzachita manyazi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa