Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 12:9 - Buku Lopatulika

9 Pamenepo mwini munda adzachita chiyani? Adzafika, nadzaononga olimawo, nadzapereka mundawo kwa ena.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Pamenepo mwini munda adzachita chiyani? Adzafika, nadzaononga olimawo, nadzapereka mundawo kwa ena.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 “Kodi mwini munda wamphesa uja adzachita chiyani? Ndithu, adzabwera naŵapha alimiwo, munda uja nkuubwereka alimi ena.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 “Kodi nanga mwini munda wamphesa adzachita chiyani? Iye adzabwera ndi kupha alimiwo nadzapereka munda wamphesawo kwa ena.

Onani mutuwo Koperani




Marko 12:9
33 Mawu Ofanana  

Kodi sikatsala kamphindi kakang'ono, ndipo Lebanoni adzasanduka munda wobalitsa, ndi munda wobalitsa udzayesedwa nkhalango?


Ndipo mudzasiya dzina lanu likhale chitemberero kwa osankhidwa anga, ndipo Ambuye Yehova adzakupha iwe, nadzatcha atumiki ake dzina lina;


Iwe phiri langa la m'munda, ndidzapereka chuma chako ndi zosungidwa zako zikafunkhidwe, ndi misanje yako, chifukwa cha tchimo, m'malire ako onse.


Pakuti kuyambira kotulukira dzuwa kufikira kolowera kwake dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu; ndipo m'malo monse adzaperekera dzina langa chofukiza ndi chopereka choona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu, ati Yehova wa makamu.


Pomwepo upita, nutenga pamodzi ndi uwu mizimu ina inzake isanu ndi iwiri yoipa yoposa mwini yekhayo, ndipo ilowa, nikhalamo. Ndipo matsirizidwe ake a munthu uyo akhala oipa oposa mayambidwe ake. Kotero kudzakhalanso kwa obadwa oipa amakono.


Ndipo pamene nyengo ya zipatso inayandikira, anatumiza akapolo ake kwa olima mundawo, kukalandira zipatso zake.


Chifukwa chake ndinena kwa inu, Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu, nudzapatsidwa kwa anthu akupatsa zipatso zake.


Koma mfumu inakwiya; nituma asilikali ake napululutsa ambanda aja, nitentha mzinda wao.


Kodi simunawerenge ngakhale lembo ili, Mwala umene anaukana omanga nyumba, womwewu unayesedwa mutu wa pangodya:


Ndipo anamtenga, namupha iye, namtaya kunja kwa munda.


Koma adani anga aja osafuna kuti ndidzakhala mfumu yao, bwerani nao kuno, nimuwaphe pamaso panga.


Ndipo Yesaya alimbika mtima ndithu, nati, Ndinapezedwa ndi iwo amene sanandifune; ndinaonekera kwa iwo amene sanandifunse.


Ndipo kudzakhala kuti monga zakugwerani zokoma zonse anakunenerani Yehova Mulungu wanu, momwemo Yehova adzakutengerani zoipa zonse mpaka atakuonongani kukuchotsani m'dziko lokoma ili anakupatsani Yehova Mulungu wanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa