Mateyu 1:25 - Buku Lopatulika ndipo sanamdziwe iye kufikira atabala mwana wake; namutcha dzina lake Yesu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo sanamdziwe iye kufikira atabala mwana wake; namutcha dzina lake Yesu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa koma sadamdziŵe mpaka adabala mwana wamwamuna. Pambuyo pake Yosefe adatcha mwanayo dzina loti Yesu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma sanagone malo amodzi mpaka mwanayo atabadwa ndipo anamutcha dzina lake Yesu. |
Ndipo namwaliyo anali wokongola ndithu, namasunga mfumu namtumikira; koma mfumu sinamdziwe.
Ndipatulire Ine yense woyamba kubadwa, wotsegulira pa amake mwa ana a Israele, mwa anthu ndi mwa zoweta; ndiwo anga.
Usachedwa kuperekako zipatso zako zochuluka, ndi zothira zako. Woyamba wa ana ako aamuna undipatse Ine.
Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake kumachimo ao.
Ndipo Yosefe anauka tulo take, nachita monga anamuuza mngelo wa Ambuye, nadzitengera yekha mkazi wake;
Ndipo taona, udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wamwamuna, nudzamutcha dzina lake Yesu.
Ndipo pamene panakwanira masiku asanu ndi atatu akumdula Iye, anamutcha dzina lake Yesu, limene anatchula mngeloyo asanalandiridwe Iye m'mimba.
Ndipo iye anabala mwana wake wamwamuna woyamba; namkulunga Iye m'nsalu, namgoneka modyera ng'ombe, chifukwa kuti anasowa malo m'nyumba ya alendo.
Chifukwa kuti iwo amene Iye anawadziwiratu, iwowa anawalamuliratu afanizidwe ndi chifaniziro cha Mwana wake, kuti Iye akakhale mwana woyamba wa abale ambiri;