tapenyani, m'mene atibwezera, kudzatiinga m'cholowa chanu, chimene munatipatsa chikhale cholowa chathu.
Masalimo 83:5 - Buku Lopatulika Pakuti anakhalira upo ndi mtima umodzi; anachita chipangano cha pa Inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti anakhalira upo ndi mtima umodzi; anachita chipangano cha pa Inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zoonadi, akumvana popangana chiwembu, akupangana zokuukirani, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndi mtima umodzi akukonzekera chiwembu; Iwo achita mgwirizano kutsutsana nanu: |
tapenyani, m'mene atibwezera, kudzatiinga m'cholowa chanu, chimene munatipatsa chikhale cholowa chathu.
Koma anachiyesa chopepuka kumthira manja Mordekai yekha; pakuti adamfotokozera mtundu wake wa Mordekai; potero Hamani anafuna kuononga Ayuda onse okhala mu ufumu wonse wa Ahasuwero, ndiwo a mtundu wa Mordekai.
Adzikhazikitsa mafumu a dziko lapansi, nachita upo akulu pamodzi, Kutsutsana naye Yehova, ndi Wodzozedwa wake, ndi kuti,
Ananena mumtima mwao, Tiwapasule pamodzi; anatentha zosonkhaniramo za Mulungu zonse, m'dzikomo.
Ndipo anauza a nyumba ya Davide, kuti Aramu wapangana ndi Efuremu. Ndipo mtima wake unagwedezeka, ndi mtima wa anthu ake, monga mitengo ya m'nkhalango igwedezeka ndi mphepo.
Kodi sulingalira chomwe anena anthu awa, kuti, Mabanja awiri amene Yehova anawasankha, wataya iwo? Chomwecho anyoza anthu anga, kuti asakhalenso mtundu pamaso pao.
Atero Ambuye Yehova, Popeza Afilisti anachita mobwezera chilango nabwezera chilango ndi mtima wopeputsa kuononga, ndi udani wosatha,
Ndipo tsopano amitundu ambiri asonkhana kuyambana nawe, akuti, Aipsidwe, diso lathu lipenye ku Ziyoni.
Akadzamva ichi Akanani ndi okhala m'dziko onse, adzatizinga ndi kuduliratu dzina lathu padziko lapansi; ndipo mudzachitiranji dzina lanu lalikulu?
Ndipo ndinaona chilombocho, ndi mafumu a dziko, ndi magulu a nkhondo ao, osonkhanidwa kuchita nkhondo pa Iye wakukwera pa kavalo, ndi gulu la nkhondo lake.