Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mika 4:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo tsopano amitundu ambiri asonkhana kuyambana nawe, akuti, Aipsidwe, diso lathu lipenye ku Ziyoni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo tsopano amitundu ambiri asonkhana kuyambana nawe, akuti, Aipsidwe, diso lathu lipenye ku Ziyoni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Tsopano mitundu yambiri yasonkhana kuti imenyane ndi iwe Ziyoni. Ikunena kuti, “Tiyeni timuipitse, tiwone kutha kwake kwa mzinda wa Ziyoniwu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Koma tsopano mitundu yambiri ya anthu yasonkhana kulimbana nawe. Iwo akuti, “Tiyeni timudetse, maso athu aone chiwonongeko cha Ziyoni!”

Onani mutuwo Koperani




Mika 4:11
15 Mawu Ofanana  

Achite manyazi nabwerere m'mbuyo. Onse akudana naye Ziyoni.


Pakuti anakhalira upo ndi mtima umodzi; anachita chipangano cha pa Inu.


Koma iye safuna chotero, ndipo mtima wake suganizira chotero, koma mtima wake ulikufuna kusakaza, ndi kuduladula amitundu osawerengeka.


Ha, phokoso la mitundu yambiri ya anthu ambiri, amene afuula ngati kukukuma kwa nyanja; ndi kuthamanga kwa amitundu, akuthamanga ngati kuthamanga kwa madzi amphamvu!


Ndipo khamu la mitundu yonse yomenyana ndi Ariyele, ngakhale yonse yomenyana naye ndi linga lake, ndi kumsautsa idzafanana ndi loto, masomphenya a usiku.


Ndipo panaoneka chaka chachisanu ndi chinai cha ufumu wake mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anafika, iye ndi nkhondo yake, kuti amenyane ndi Yerusalemu, ndipo anammangira zithando; ndipo anammangira malinga pozungulira pake.


chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona ndikutsutsa iwe, Tiro, ndidzakukweretsera amitundu, monga nyanja iutsa mafunde ake.


Atero Ambuye Yehova, Kodi iwe ndiwe iye amene ndinanena za iye masiku akale mwa atumiki anga aneneri a Israele, akunenera masiku aja za zaka za m'tsogolo, kuti ndidzabwera nawe kulimbana nao?


Koma usapenyerera tsiku la mphwako, tsiku loyesedwa mlendo iye, nusasekerere ana a Yuda tsiku la kuonongeka kwao, kapena kuseka chikhakha tsiku lakupsinjika.


Pamenepo mdani wanga adzachiona, ndi manyazi adzamkuta iye amene adati kwa ine, Ali kuti Yehova Mulungu wako? Maso anga adzamuona; tsopano adzampondereza ngati thope la m'miseu.


Ndipo kudzachitika tsiku ilo, ndidzaika Yerusalemu akhale mwala wolemetsa mitundu yonse ya anthu; onse akuusenza adzadzilasa nao; ndi amitundu onse a padziko lapansi adzasonkhana kutsutsana nao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa