Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mika 4:10 - Buku Lopatulika

10 Imva zowawa, nuyesetse kubala, mwana wamkazi wa Ziyoni, ngati mkazi wakubala; pakuti udzatuluka m'mzinda tsopano, nudzakhala kuthengo, nudzafika ku Babiloni; komweko udzapulumutsidwa; komweko Yehova adzakuombola m'manja a adani ako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Imva zowawa, nuyesetse kubala, mwana wamkazi wa Ziyoni, ngati mkazi wakubala; pakuti udzatuluka m'mudzi tsopano, nudzakhala kuthengo, nudzafika ku Babiloni; komweko udzapulumutsidwa; komweko Yehova adzakuombola m'manja a adani ako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Muphiriphithe ndi kubuula, inu anthu a ku Ziyoni, ngati mkazi pa nthaŵi yake yochira. Pakuti tsopano mudzachoka mumzindamo, mukakhala mumidzi. Mudzachotsedwa kupita ku Babiloni. Komabe kumeneko mudzapulumutsidwa, kumeneko Chauta adzakuwombolani kwa adani anu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Gubuduka ndi ululu, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni, ngati mayi pa nthawi yake yobereka, pakuti tsopano muyenera kuchoka mu mzinda ndi kugona kunja kwa mzindawo. Udzapita ku Babuloni; kumeneko udzapulumutsidwa, kumeneko Yehova adzakuwombola mʼmanja mwa adani ako.

Onani mutuwo Koperani




Mika 4:10
27 Mawu Ofanana  

Nadzatenga ena a ana ako otuluka mwa iwe, amene udzawabala, nadzakhala iwo adindo m'chinyumba cha mfumu ya Babiloni.


Pamenepo linga la mzindawo linagamulidwa, nathawira ankhondo onse usiku, njira ya ku chipata cha pakati pa makoma awiri, ili ku munda wa mfumu; Ababiloni tsono anali pamzinda pouzinga; nimuka mfumu panjira ya kuchidikha.


Motero Yehova anawafikitsira akazembe a khamu la nkhondo la mfumu ya Asiriya, namgwira Manase ndi zokowera, nammanga matangadza, namuka naye ku Babiloni.


Ndi iwo amene adapulumuka kulupanga anamuka nao ku Babiloni, nakhala iwo anyamata ake, ndi a ana ake, mpaka mfumu ya Persiya idachita ufumu;


Atero Kirusi mfumu ya Persiya, Yehova Mulungu Wam'mwamba anandipatsa maufumu onse a padziko lapansi nandilangiza ndimmangire nyumba mu Yerusalemu, ndiwo ku Yuda. Aliyense mwa inu a anthu ake onse, Yehova Mulungu wake akhale naye, akwereko.


Ndipo anawapulumutsa m'dzanja la iye amene anawada, nawaombola kudzanja la mdani.


Atero Yehova, Mombolo wanu, Woyera wa Israele: Chifukwa cha inu ndatumiza ku Babiloni, ndipo ndidzatsitsira iwo onse monga othawa, ngakhale Ababiloni m'ngalawa za kukondwa kwao.


Ine ndautsa Kirusi m'chilungamo, ndipo ndidzalungamitsa njira zake zonse; iye adzamanga mzinda wanga, nadzaleka andende anga anke mwaufulu, wosati ndi mtengo pena mphotho, ati Yehova wa makamu.


Tulukani inu mu Babiloni, athaweni Ababiloni; ndi mau akuimba nenani inu, bukitsani ichi, lalikirani ichi, ngakhale ku malekezero a dziko; nenani, Yehova waombola mtumiki wake Yakobo.


Tenga mpango umene unaugula, umene uli m'chuuno mwako, nuuke, nupite ku Yufurate, nuubise m'menemo m'phanga la m'mwala.


Ndipo ndidzakulanditsa iwe m'dzanja la oipa, ndipo ndidzakuombola iwe m'dzanja la oopsa.


Pamenepo tamvani inu mau a Yehova, inu nonse a m'ndende, amene ndachotsa mu Yerusalemu kunka ku Babiloni.


Pakuti ndamva kubuula ngati kwa mkazi wobala, ndi msauko ngati wa mkazi wobala mwana wake woyamba, mau a mwana wamkazi wa Ziyoni wakupuma mosiyiza, wakutambasula manja ake, ndi kuti, Tsoka ine tsopano! Pakuti moyo wanga walefuka chifukwa cha ambanda.


Keriyoti walandidwa, ndi malinga agwidwa, ndipo tsiku lomwelo mtima wa anthu amphamvu a Mowabu adzakhala ngati mtima wa mkazi alinkudwala.


Ndipo mfumu ya ku Babiloni anawakantha, nawapha pa Ribula m'dziko la Hamati. Chomwecho Yuda anatengedwa ndende kutuluka m'dziko lake.


Angakhale anatero, kuwerenga kwake kwa ana a Israele kudzanga mchenga wa kunyanja, wosayeseka kapena kuwerengeka; ndipo kudzatero kuti m'mene adawanena, Simuli anthu anga, adzanena nao, Muli ana a Mulungu wamoyo.


Zowawa zonga za mkazi wobala zidzamgwera, ndiye mwana wopanda nzeru; pakuti pali nyengo yakuti asachedwe mobalira ana.


Chifukwa chake taonani, ndidzamkopa ndi kunka naye kuchipululu, ndi kulankhula naye momkonda mtima.


Koma iwe, Betelehemu Efurata, ndiwe wamng'ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditulukira wina wakudzakhala woweruza mu Israele; matulukiro ake ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.


Chifukwa chake Iye adzawapereka kufikira nthawi yoti wobalayo wabala; pamenepo otsala a abale ake adzabwera pamodzi ndi ana a Israele.


Ndipo anapatsa mkazi mapiko awiri a chiombankhanga chachikulu, kuti akaulukire kuchipululu, ku mbuto yake, kumene adyetsedwako nthawi, ndi zinthawi, ndi nusu la nthawi, osapenya nkhope ya njoka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa