Ndidzakuyamikani ndi mtima wanga wonse; ndidzaimba zakukulemekezani patsogolo pa milungu.
Masalimo 82:1 - Buku Lopatulika Mulungu aima mu msonkhano wa Mulungu, aweruza pakati pa milungu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mulungu aima mu msonkhano wa Mulungu, aweruza pakati pa milungu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu akutsogolera msonkhano wakumwamba. Akugamula mlandu milungu ya pansi pano. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mulungu akutsogolera msonkhano waukulu; Iye akuweruza pakati pa “milungu.” |
Ndidzakuyamikani ndi mtima wanga wonse; ndidzaimba zakukulemekezani patsogolo pa milungu.
Mulungu wa milungu, Yehova, wanena, aitana dziko lapansi kuyambira kutuluka kwa dzuwa kufikira kulowa kwake.
Ndipo anthu adzati, Indedi, pali mphotho kwa wolungama. Indedi, pali Mulungu wakuweruza padziko lapansi.
Inde, mumtima muchita zosalungama; padziko lapansi mugawira anthu chiwawa cha m'manja mwanu.
Koma iwe, dzisankhire mwa anthu ako onse, amuna anzeru, akuopa Mulungu, amuna oona, akudana nalo phindu la chinyengo; nuwaikire iwo oterewa, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, akulu a pa makumi;
pamenepo mbuye wake azifika naye kwa oweruza, nafike naye kukhomo, kapena kumphuthu, ndipo mbuye wake am'boole khutu lake ndi lisungulo; ndipo iye azimgwirira ntchito masiku onse.
Ukaona anthu alikutsendereza aumphawi, ndi kuchotsa chilungamo ndi chiweruzo mwachiwawa pa dera lina la dziko, usazizwepo; pakuti mkulu wopambana asamalira; ndipo alipo akulu ena oposa amenewo.
Ngati anawatcha milungu iwo amene mau a Mulungu anawadzera (ndipo cholemba sichingathe kuthyoka),