Imvani, anthu anga, ndipo ndidzanena; Israele, ndipo ndidzachita mboni pa iwe, Ine Mulungu, ndine Mulungu wako.
Masalimo 81:8 - Buku Lopatulika Tamvani, anthu anga, ndidzakuchitirani mboni; Israele, ukadzandimvera! Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tamvani, anthu anga, ndidzakuchitirani mboni; Israele, ukadzandimvera! Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Imvani inu anthu anga, ndikulangizeni. Inu Aisraele, chonde mukadandimvera! Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Imvani anthu anga, ndipo ndidzakuchenjezani ngati mungathe kumvetsera, Inu Israeli! |
Imvani, anthu anga, ndipo ndidzanena; Israele, ndipo ndidzachita mboni pa iwe, Ine Mulungu, ndine Mulungu wako.
ndipo anati, Ngati udzamveratu mau a Yehova, Mulungu wako, ndi kuchita zoona pamaso pake, ndi kutchera khutu pa malamulo ake, ndi kusunga malemba ake onse, za nthenda zonse ndinaziika pa Aejipito sindidzaziika pa iwe nnena imodzi; pakuti Ine Yehova ndine wakuchiritsa iwe.
Ndipo anatcha dzina la malowo Masa, ndi Meriba, chifukwa cha kutsutsana kwa ana a Israele; popezanso anayesa Yehova, ndi kuti, Kodi Yehova ali pakati pa ife, kapena iai?
Ndipo kunali tsiku lachitatu, m'mawa, panali mabingu ndi zimphezi, ndi mtambo wakuda bii paphiripo, ndi liu la lipenga lolimbatu; ndi anthu onse okhala kutsasa ananjenjemera.
Awa ndi madzi a Meriba; popeza ana a Israele anatsutsana ndi Yehova, ndipo anapatulidwa mwa iwowa.
Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, Tilankhula chimene tichidziwa, ndipo tichita umboni za chimene tachiona; ndipo umboni wathu simuulandira.
ndi kuchitira umboni Ayuda ndi Agriki wa kutembenuka mtima kulinga kwa Mulungu, ndi chikhulupiriro cholinga kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.
nati nao, Ikani mitima yanu pa mau onse ndikuchitirani nao mboni lero; kuti muuze ana anu asamalire kuwachita mau onse a chilamulo ichi.
Yandikizani inu, ndi kumva zonse Yehova Mulungu wathu adzati; ndipo inu munene ndi ife zonse zimene Yehova Mulungu wathu adzanena ndi inu; ndipo ife tidzazimva ndi kuzichita.
Ngati tilandira umboni wa anthu, umboni wa Mulungu uposa; chifukwa umboni wa Mulungu ndi uwu, kuti anachita umboni za Mwana wake.