Ndipo Melkizedeki mfumu ya ku Salemu, anatuluka nao mkate ndi vinyo: iye ndiye wansembe wa Mulungu Wamkulukulu.
Masalimo 76:2 - Buku Lopatulika Msasa wake unali mu Salemu, ndipo pokhala Iye mu Ziyoni. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Msasa wake unali m'Salemu, ndipo pokhala Iye m'Ziyoni. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Hema lake adalimanga ku Yerusalemu. Malo ake okhalamo ali kumeneko ku Ziyoni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tenti yake ili mu Salemu, malo ake okhalamo mu Ziyoni. |
Ndipo Melkizedeki mfumu ya ku Salemu, anatuluka nao mkate ndi vinyo: iye ndiye wansembe wa Mulungu Wamkulukulu.
Koma ndinasankha Yerusalemu, kuti dzina langa likhale komweko; ndinasankhanso Davide akhale mfumu ya anthu anga Israele.
Chifukwa kuti pa tsiku la tsoka Iye adzandibisa mumsasa mwake, adzandibisa mkati mwa chihema chake; pathanthwe adzandikweza.
Phiri la Ziyoni, chikhalidwe chake nchokoma kumbali zake za kumpoto, ndilo chimwemwe cha dziko lonse lapansi, mzinda wa mfumu yaikulu.
Tafuula, takuwa iwe, wokhala mu Ziyoni, chifukwa Woyera wa Israele wa m'kati mwako ali wamkulu.
Wachotsa mwamphamvu dindiro lake ngati la m'munda; waononga mosonkhanira mwake; Yehova waiwalitsa anthu msonkhano ndi Sabata mu Ziyoni; wanyoza mfumu ndi wansembe mokwiya mwaukali.