Maliro 2:6 - Buku Lopatulika6 Wachotsa mwamphamvu dindiro lake ngati la m'munda; waononga mosonkhanira mwake; Yehova waiwalitsa anthu msonkhano ndi Sabata mu Ziyoni; wanyoza mfumu ndi wansembe mokwiya mwaukali. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Wachotsa mwamphamvu dindiro lake ngati la m'munda; waononga mosonkhanira mwake; Yehova waiwalitsa anthu msonkhano ndi Sabata m'Ziyoni; wanyoza mfumu ndi wansembe mokwiya mwaukali. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Adapasula Nyumba yake ngati khumbi lam'munda, malo ake a msonkhano adaŵasandutsa bwinja. Chauta adathetseratu ku Ziyoni masiku achikondwerero ndi a Sabata. Ndipo atakwiya kwambiri adanyoza mfumu pamodzi ndi ansembe. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Wagwetsa malo ake okhalamo ngati khumbi la mʼmunda; wawononga malo ake a msonkhano. Yehova wayiwalitsa Ziyoni maphwando ake oyikika ndi masabata ake. Mokwiya kwambiri, Iye ananyoza mfumu ndi wansembe. Onani mutuwo |
Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Monga mkwiyo wanga ndi ukali wanga wathiridwa kwa okhala mu Yerusalemu, momwemo ukali wanga udzathiridwa pa inu, pamene mudzalowa mu Ejipito; ndipo mudzakhala chitukwano, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, ndi chitonzo; ndipo simudzaonananso malo ano.