Iye adzakhala ngati kuunika kwa m'mawa, potuluka dzuwa, M'mawa mopanda mitambo; pamene msipu uphuka kutuluka pansi, chifukwa cha kuwala koyera, italeka mvula.
Masalimo 72:6 - Buku Lopatulika Adzanga mvula yakugwa pa udzu wosenga, monga mvula yothirira dziko. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Adzanga mvula yakugwa pa udzu wosenga, monga mvula yothirira dziko. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Idzakhala madalitso ngati mvula yogwa pa minda ngati mvula yowaza pa nthaka! Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye adzakhala kugwa kwa mvula pa minda yolimidwa ngati mivumbi yothirira dziko lapansi. |
Iye adzakhala ngati kuunika kwa m'mawa, potuluka dzuwa, M'mawa mopanda mitambo; pamene msipu uphuka kutuluka pansi, chifukwa cha kuwala koyera, italeka mvula.
Mukhutitsa nthaka yake yolima; mufafaniza nthumbira zake; muiolowetsa ndi mvumbi; mudalitsa mmera wake.
M'kuunika kwa nkhope ya mfumu muli moyo; kukoma mtima kwake kunga mtambo wa mvula ya masika.
Mkwiyo wa mfumu ukunga kubangula kwa mkango; koma kukoma mtima kwake kunga mame pamsipu.
ndipo ndidzaupasula; sudzadzomboleredwa kapena kulimidwa; koma padzamera lunguzi ndi minga; ndidzalamuliranso mitambo kuti isavumbwepo mvula.
Tidziwe tsono, tilondole kudziwa Yehova; kutuluka kwake kwakonzekeratu ngati matanda kucha; ndipo adzatidzera ngati mvula, ngati mvula ya masika yakuthirira dziko.
Ndipo iwo adzatha dziko la Asiriya ndi lupanga, ndi dziko la Nimirodi, ndilo polowera pake; ndipo adzatilanditsa kwa a ku Asiriya pamene alowa m'dziko lathu, pamene aponda m'kati mwa malire athu.
Chiphunzitso changa chikhale ngati mvula; maneno anga agwe ngati mame; ngati mvula yowaza pamsipu, ndi monga madontho a mvula pazitsamba.