Adani anga asandikondwerere ine monyenga; okwiya nane kopanda chifukwa asanditsinzinire.
Masalimo 69:4 - Buku Lopatulika Ondida kopanda chifukwa achuluka koposa tsitsi la pamutu panga; ofuna kunditha, ndiwo adani anga monama, ali ndi mphamvu. Pamenepo andibwezetsa chosafunkha ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ondida kopanda chifukwa achuluka koposa tsitsi la pamutu panga; ofuna kunditha, ndiwo adani anga monama, ali ndi mphamvu. Pamenepo andibwezetsa chosafunkha ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu odana nane popanda chifukwa ndi ochuluka kupambana tsitsi la kumutu kwanga. Ndi amphamvu anthu ongofuna kundiwononga, ndi kundineneza ndi mabodza ao. Kodi ndiyenera kubweza zimene sindinabe? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo amene amadana nane popanda chifukwa ndi ochuluka kuposa tsitsi la kumutu kwanga; ambiri ndi adani anga popanda chifukwa, iwo amene akufunafuna kundiwononga. Ndikukakamizidwa kubwezera zomwe sindinabe. |
Adani anga asandikondwerere ine monyenga; okwiya nane kopanda chifukwa asanditsinzinire.
Pakuti zoipa zosawerengeka zandizinga, zochimwa zanga zandipeza kotero kuti sindikhoza kupenya; ziposa tsitsi la mutu wanga, ndipo wandichokera mtima.
Pakuti onani, alalira moyo wanga; amphamvu andipangira chiwembu, osachimwa, osalakwa ine, Yehova,
Koma chitero, kuti mau olembedwa m'chilamulo chao akwaniridwe, kuti, Anandida Ine kopanda chifukwa.
Ameneyo sanadziwe uchimo anamyesera uchimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.
amene anasenza machimo athu mwini yekha m'thupi mwake pamtanda, kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo; ameneyo mikwingwirima yake munachiritsidwa nayo.
Pakuti Khristunso adamva zowawa kamodzi, chifukwa cha machimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m'thupi, koma wopatsidwa moyo mumzimu;