Masalimo 61:3 - Buku Lopatulika Pakuti munakhala pothawirapo panga; nsanja yolimba pothawa mdani ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti munakhala pothawirapo panga; nsanja yolimba pothawa mdani ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inutu ndinu kothaŵira kwanga, nsanja yolimba yonditeteza kwa adani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti Inu mwakhala pothawirapo panga, nsanja yolimba polimbana ndi adani anga. |
Yehova Ambuye, ndinu mphamvu ya chipulumutso changa, munandiphimba mutu wanga tsiku lakulimbana nkhondo.
Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye; chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.
Chifukwa kuti pa tsiku la tsoka Iye adzandibisa mumsasa mwake, adzandibisa mkati mwa chihema chake; pathanthwe adzandikweza.
Pa Mulungu pali chipulumutso changa ndi ulemerero wanga. Thanthwe la mphamvu yanga ndi pothawirapo panga mpa Mulungu.
amene anatilanditsa mu imfa yaikulu yotere, nadzalanditsa; amene timyembekezera kuti adzalanditsanso;