Masalimo 41:4 - Buku Lopatulika Ndinati ine, Mundichitire chifundo, Yehova; Chiritsani mtima wanga; pakuti ndachimwira Inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndinati ine, Mundichitire chifundo, Yehova; Chiritsani mtima wanga; pakuti ndachimwira Inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ndidati, “Inu Chauta, ndakuchimwirani, mundikomere mtima, muchiritse moyo wanga.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndinati, “Inu Yehova, mundichitire chifundo; chiritseni pakuti ndakuchimwirani.” |
Ndinavomera choipa changa kwa Inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibise. Ndinati, Ndidzaululira Yehova machimo anga; ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.
Tiyeni, tibwerere kunka kwa Yehova; pakuti wang'amba, nadzatipoletsera; wakantha, nadzatimanga.