Ndipo Abisalomu, ndi anthu onse aamuna a Israele, anafika ku Yerusalemu, ndi Ahitofele pamodzi naye.
Masalimo 3:1 - Buku Lopatulika Yehova! Ha! Achuluka nanga akundisautsa ine! Akundiukira ine ndi ambiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova! Ha! Achuluka nanga akundisautsa ine! Akundiukira ine ndi ambiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu Chauta, ndili ndi adani ochuluka, anthu ambiri akundiwukira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu Yehova, achulukadi adani anga! Achulukadi amene andiwukira! |
Ndipo Abisalomu, ndi anthu onse aamuna a Israele, anafika ku Yerusalemu, ndi Ahitofele pamodzi naye.
Onetsani chifundo chanu chodabwitsa, Inu wakupulumutsa okhulupirira Inu kwa iwo akuwaukira ndi dzanja lanu lamanja.
Ndipo mbale adzapereka mbale wake kuimfa, ndi atate mwana wake: ndipo ana adzatsutsa akuwabala, nadzawafetsa iwo.
Ndipo mafumu awa onse anasonkhana, nadza namanga pamodzi ku madzi a Meromu, kumthira Israele nkhondo.