Masalimo 26:4 - Buku Lopatulika Sindinakhala pansi ndi anthu achabe; kapena kutsagana nao anthu othyasika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Sindinakhala pansi ndi anthu achabe; kapena kutsagana nao anthu othyasika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Sindikhala pamodzi ndi anthu onyenga, sindiyenda ndi anthu achiphamaso. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ine sindikhala pansi pamodzi ndi anthu achinyengo, kapena kufunsa nzeru kwa achiphamaso. |
Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa, kapena wosaimirira m'njira ya ochimwa, kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza.
Sindinakhala m'msonkhano wa iwo amene asekerasekera, ndi kusangalala; ndinakhala pandekha chifukwa cha dzanja lanu; pakuti mwandidzaza ndi mkwiyo.
Chifukwa chake, Tulukani pakati pao, ndipo patukani, ati Ambuye, Ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka; ndipo Ine ndidzalandira inu,