Masalimo 22:3 - Buku Lopatulika Koma Inu ndinu woyera, wakukhala m'malemekezo a Israele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Inu ndinu woyera, wakukhala m'malemekezo a Israele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Komabe Inu ndinu oyera, mumakhala pa mpando wanu waufumu, ndipo anthu anu Aisraele amakutamandani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu ndinu Woyera, wokhala pa mpando waufumu; ndinu matamando a Israeli. |
Wopereka nsembe yachiyamiko andilemekeza Ine; ndipo kwa iye wosunga mayendedwe ake ndidzamuonetsa chipulumutso cha Mulungu.
Mkwezeni Yehova Mulungu wathu, ndipo gwadirani paphiri lake loyera; pakuti Yehova Mulungu wathu ndiye woyera.
Ndipo wina anafuula kwa mnzake, nati, Woyera, Woyera, Woyera, Yehova wa makamu; dziko lonse lapansi ladzala ulemerero wake.
Yehova, ndidzafuula mpaka liti osamva Inu? Ndifuulira kwa Inu za chiwawa, koma simupulumutsa.
Iye ndiye lemekezo lanu, Iye ndiye Mulungu wanu, amene anachita nanu zazikulu ndi zoopsa izi, mudaziona m'maso mwanu.
Ndipo zamoyozo zinai, chonse pa chokha chinali nao mapiko asanu ndi limodzi; ndipo zinadzala ndi maso pozinga ponse ndi m'katimo; ndipo sizipumula usana ndi usiku, ndi kunena, Woyera, woyera, woyera, Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, amene anali, amene ali, ndi amene alinkudza.