Motero mwazi wao udzabweranso pamutu wake wa Yowabu, ndi pamutu wa mbumba yake, ku nthawi yamuyaya; koma Davide, ndi mbumba yake, ndi banja lake, ndi mpando wake wachifumu adzakhala ndi mtendere wa Yehova ku nthawi yamuyaya.
Masalimo 21:4 - Buku Lopatulika Anakupemphani moyo, mwampatsa iye; mwamtalikitsira masiku kunthawi za nthawi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anakupemphani moyo, mwampatsa iye; mwamtalikitsira masiku kunthawi za nthawi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iyo idakupemphani moyo, ndipo Inu mudaipatsa moyo wautali, wamuyaya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anakupemphani moyo, ndipo munamupatsa masiku ochuluka kwamuyaya. |
Motero mwazi wao udzabweranso pamutu wake wa Yowabu, ndi pamutu wa mbumba yake, ku nthawi yamuyaya; koma Davide, ndi mbumba yake, ndi banja lake, ndi mpando wake wachifumu adzakhala ndi mtendere wa Yehova ku nthawi yamuyaya.
Koma mfumu Solomoni adzadalitsika, ndi mpando wachifumu wa Davide udzakhazikika pamaso pa Yehova ku nthawi yamuyaya.
Atatero, anatulutsa mwana wa mfumu, namuika korona, nampatsa buku la umboni, namlonga ufumu, namdzoza, naomba m'manja, nati, Mfumu ikhale ndi moyo.
Nsoni zokoma zanu zindidzere, kuti ndikhale ndi moyo; popeza chilamulo chanu chindikondweretsa.
Penyani, ndiyankheni, Yehova Mulungu wanga. Penyetsani maso anga, kuti ndingagone tulo ta imfa;
Ngati mame a ku Heremoni, akutsikira pa mapiri a Ziyoni. Pakuti pamenepo Yehova analamulira dalitsolo, ndilo moyo womka muyaya.
Dzina lake lidzakhala kosatha, momwe likhalira dzuwa dzina lake lidzamvekera zidzukulu. Ndipo anthu adzadalitsidwa mwa Iye; amitundu onse adzamutcha wodala.
Ndidzakhalitsanso mbeu yake chikhalire, ndi mpando wachifumu wake ngati masiku a m'mwamba.
inde adzamanga Kachisi wa Yehova; nadzasenza ulemererowo, nadzakhala ndi kulamulira pa mpando wachifumu wake; nadzakhala wansembe pampando wachifumu wake; ndi uphungu wa mtendere udzakhala pakati pa iwo awiri.
ndi Wamoyoyo; ndipo ndinali wakufa, ndipo taona, ndili wamoyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo ndili nazo zofungulira za imfa ndi dziko la akufa.