Ndiponso Abele anatenga iyenso mwana woyamba wa nkhosa zake ndi mafuta omwe. Yehova ndipo anayang'anira Abele ndi nsembe yake:
Masalimo 20:3 - Buku Lopatulika likumbukire zopereka zako zonse, lilandire nsembe yako yopsereza; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 likumbukire zopereka zako zonse, lilandire nsembe yako yopsereza; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Alandire zopereka zako zonse, akondwere ndi nsembe zako zopsereza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye akumbukire nsembe zako zonse ndipo alandire nsembe zako zopsereza. Sela |
Ndiponso Abele anatenga iyenso mwana woyamba wa nkhosa zake ndi mafuta omwe. Yehova ndipo anayang'anira Abele ndi nsembe yake:
Ndipo Davide anamangira Yehova guwa la nsembe komweko; napereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika, naitana kwa Yehova; ndipo anamyankha ali m'mwamba ndi moto paguwa la nsembe yopsereza.
Atatha tsono Solomoni kupemphera, moto unatsika kumwamba, nunyeketsa nsembe yopsereza, ndi nsembe zophera; ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza nyumbayi.
Yehova adzakudalitsa ali mu Ziyoni; ndipo udzaona zokoma za Yerusalemu masiku onse a moyo wako.
Pamenepo mudzakondwera nazo nsembe zachilungamo, ndi nsembe yopsereza ndi yopsereza yathunthu; pamenepo adzapereka ng'ombe paguwa lanu la nsembe.
Zoweta za Kedara zidzasonkhana kwa iwe, nkhosa zamphongo za Nebayoti zidzakutumikira; izo zidzafika ndi kulandiridwa paguwa langa la nsembe; ndipo ndidzakometsa nyumba ya ulemerero wanga.
Ndipo unatuluka moto pamaso ya Yehova, nunyeketsa nsembe yopsereza ndi mafuta paguwa la nsembe; ndipo pakuchiona anthu onse anafuula, nagwa nkhope zao pansi.
Ndipo pompenyetsetsa iye ndi kuopa, anati, Nchiyani, Mbuye? Ndipo anati kwa iye, Mapemphero ako ndi zachifundo zako zinakwera zikhala chikumbutso pamaso pa Mulungu.
ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.
inunso ngati miyala yamoyo mumangidwa nyumba ya uzimu, kuti mukhale ansembe oyera mtima, akupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa Yesu Khristu.