Ndipo mwana wamkazi wa Tiro adzafika nayo mphatso; achuma a mwa anthu adzapempha kudziwika nanu.
Masalimo 2:10 - Buku Lopatulika Tsono, mafumu inu, chitani mwanzeru; langikani, oweruza inu a dziko lapansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tsono, mafumu inu, chitani mwanzeru; langikani, oweruza inu a dziko lapansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nchifukwa chake tsono khalani anzeru, inu mafumu. Chenjerani inu amene muli olamula dziko lapansi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kotero, inu mafumu, chenjerani; chenjezedwani, inu olamulira a dziko lapansi. |
Ndipo mwana wamkazi wa Tiro adzafika nayo mphatso; achuma a mwa anthu adzapempha kudziwika nanu.
Ndipo mafumu adzakulera, ndi akazi ao aakulu adzakuyamwitsa; iwo adzakugwadira ndi nkhope zao zoyang'ana pansi, nadzaseteka fumbi la m'mapazi ako: ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndi iwo amene alindira Ine sadzakhala ndi manyazi.
momwemonso Iye adzawazawaza mitundu yambiri; mafumu adzamtsekera Iye pakamwa pao; pakuti chimene sichinauzidwe kwa iwo adzachiona, ndi chimene iwo sanamve adzazindikira.
Ulangizidwe, Yerusalemu, ungakuchokere moyo wanga, ndingakuyese iwe bwinja, dziko losakhalamo anthu.
Wanzeru ndani, kuti azindikire izi? Waluntha, kuti adziwe izi? Pakuti njira za Yehova zili zoongoka; ndipo olungama adzayendamo, koma olakwa adzagwamo.
Ndipo kudzachitika kuti aliyense wa mabanja a dziko wosakwera kunka ku Yerusalemu kulambira mfumu Yehova wa makamu, pa iwowa sipadzakhala mvula.