Masalimo 19:1 - Buku Lopatulika Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zakumwamba zimalalika ulemerero wa Mulungu, thambo limasonyeza ntchito za manja ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zakumwamba zimalengeza za ulemerero wa Mulungu; thambo limalalikira ntchito za manja ake. |
Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova; koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.
Zakumwamba zinalengedwa ndi mau a Yehova; ndipo ndi mpweya wa m'kamwa mwake khamu lao lonse.
Ndipo zakumwamba zionetsera chilungamo chake; pakuti Mulungu mwini wake ndiye woweruza.
Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika,
Ndipo aphunzitsi adzawala ngati kunyezimira kwa thambo; ndi iwo otembenuza ambiri atsate chilungamo ngati nyenyezi kunthawi za nthawi.