Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 18:50 - Buku Lopatulika

50 Alanditsa mfumu yake ndi chipulumutso chachikulu; nachitira chifundo wodzozedwa wake, Davide, ndi mbumba yake, kunthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

50 Alanditsa mfumu yake ndi chipulumutso chachikulu; nachitira chifundo wodzozedwa wake, Davide, ndi mbumba yake, kunthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

50 Mulungu amathandiza mfumu yake, kuti izipambana nthaŵi ndi nthaŵi. Amaonetsa chikondi chake chosasinthika kwa wodzozedwa wake, ndiye kuti kwa Davide ndi kwa zidzukulu zake mpaka muyaya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

50 Iye amapereka chipambano chachikulu kwa mfumu yake; amaonetsa chikondi chosasinthika kwa wodzozedwa wake, kwa Davide ndi zidzukulu zake kwamuyaya.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 18:50
20 Mawu Ofanana  

Iye adzamangira dzina langa nyumba, ndipo ndidzakhazikitsa chimpando cha ufumu wake ku nthawi zonse.


chakukomerani kudalitsa nyumba ya mtumiki wanu, kuti ikhalebe kosatha pamaso panu; pakuti Inu Yehova mwadalitsa, ndipo idzadalitsika kosatha.


Chifukwa cha Davide mtumiki wanu musabweze nkhope ya wodzozedwa wanu.


Ndiye amene apatsa mafumu chipulumutso: Amene alanditsa Davide mtumiki wake kulupanga loipa.


Koma Ine ndadzoza mfumu yanga Pa Ziyoni, phiri langa loyera.


Pakuti chifundo chanu nchachikulu kufikira m'mwamba, ndi choonadi chanu kufikira mitambo.


Ndipo Iye anatikwezera ife nyanga ya chipulumutso, mwa fuko la Davide mwana wake.


wakunena za Mwana wake, amene anabadwa, wa mbeu ya Davide, monga mwa thupi,


Pakuti mphatso zake ndi kuitana kwake kwa Mulungu sizilapika.


Ndipo malonjezano ananenedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake. Sanena, Ndipo kwa zimbeu, ngati kunena zambiri; komatu ngati kunena imodzi, Ndipo kwa mbeu yako, ndiye Khristu.


Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Iwe ukuti ulire chifukwa cha Saulo nthawi yotani, popeza Ine ndinamkana kuti asakhale mfumu ya Israele? Dzaza nyanga yako ndi mafuta, numuke, ndidzakutumiza kwa Yese wa ku Betelehemu; pakuti ndinadzionera mfumu pakati pa ana ake.


Otsutsana ndi Yehova adzaphwanyika; kumwamba Iye adzagunda pa iwo; Yehova adzaweruza malekezero a dziko. Ndipo adzapatsa mphamvu mfumu yake, nadzakweza nyanga ya wodzozedwa wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa