Akachimwira Inu, popeza palibe munthu wosachimwa, ndipo mukakwiya nao ndi kuwapereka kwa adani, kuti iwo awatenge ndende kunka nao ku dziko la adani, ngati kutali kapena kufupi,
Masalimo 143:2 - Buku Lopatulika Ndipo musaitane mlandu wa mtumiki wanu; pakuti pamaso panu sipadzakhala wolungama wamoyo mmodzi yense. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo musaitane mlandu wa mtumiki wanu; pakuti pamaso panu sipadzakhala wolungama wamoyo mmodzi yense. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Musandizenge mlandu ine mtumiki wanu, popeza kuti palibe munthu wamoyo amene ali wolungama pamaso panu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Musazenge mlandu mtumiki wanu, pakuti palibe munthu wamoyo amene ndi wolungama pamaso panu. |
Akachimwira Inu, popeza palibe munthu wosachimwa, ndipo mukakwiya nao ndi kuwapereka kwa adani, kuti iwo awatenge ndende kunka nao ku dziko la adani, ngati kutali kapena kufupi,
Potero munthu akhala bwanji wolungama kwa Mulungu? Kapena wobadwa ndi mkazi akhala woyera bwanji?
Kodi munthu adzakhala wolungama ndi kuposa Mulungu? Kodi munthu adzakhala woyera woposa Mlengi wake?
wakusungira anthu osawerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa; koma wosamasula wopalamula; wakulanga ana ndi zidzukulu chifukwa cha mphulupulu ya atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai.
chifukwa kuti pamaso pake palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi ntchito za lamulo; pakuti uchimo udziwika ndi lamulo.
koma podziwa kuti munthu sayesedwa wolungama pa ntchito ya lamulo, koma mwa chikhulupiriro cha Yesu Khristu, ifedi tinakhulupirira kwa Khristu Yesu, kuti tikayesedwe olungama ndi chikhulupiriro cha Khristu, ndipo si ndi ntchito za lamulo; pakuti palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi ntchito za lamulo.