Ndipo pakutuluka malirowo, Davide anatumiza munthu namtenga afike kwao kunyumba yake; ndipo iyeyo anakhala mkazi wake nambalira mwana wamwamuna. Koma Yehova anaipidwa ndi chinthu chimene Davide adachita.
Masalimo 139:3 - Buku Lopatulika Muyesa popita ine ndi pogona ine, ndi njira zanga zonse muzolowerana nazo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Muyesa popita ine ndi pogona ine, ndi njira zanga zonse muzolowerana nazo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mumandipenyetsetsa ndikamayenda ndiponso ndikamagona, mumadziŵa njira zanga zonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mumapenyetsetsa pamene ndikutuluka ndi kugona kwanga; mumadziwa njira zanga zonse. |
Ndipo pakutuluka malirowo, Davide anatumiza munthu namtenga afike kwao kunyumba yake; ndipo iyeyo anakhala mkazi wake nambalira mwana wamwamuna. Koma Yehova anaipidwa ndi chinthu chimene Davide adachita.
Ndipo anaika maboma mu Edomu; m'dziko lonse la Edomu anaika maboma, ndipo Aedomu onse anasanduka anthu a Davide. Ndipo Yehova anasunga Davide kulikonse anamukako.
Pakuti Mulungu adzanena mlandu wa zochita zonse, ndi zobisika zonse, ngakhale zabwino ngakhale zoipa.
Tsoka kwa iwo amene afunitsa kubisira Yehova uphungu wao, ndi ntchito zao zili mumdima, ndipo amati ndani ationa ife? Ndani atidziwa ife?
Kodi munthu angathe kubisala mobisika kuti ndisamuone iye? Ati Yehova. Kodi Ine sindidzala kumwamba ndi dziko lapansi? Ati Yehova.
chouluzira chake chili m'dzanja lake, ndipo adzayeretsa padwale pake; ndipo adzasonkhanitsa tirigu wake m'nkhokwe, koma mankhusu adzatentha ndi moto wosazima.
Ndipo pokhala pamgonero, mdierekezi adatha kuika mu mtima wake wa Yudasi mwana wa Simoni Iskariote, kuti akampereke Iye,
Yesu m'mene adanena izi, anavutika mumzimu, nachita umboni, nati, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, kuti mmodzi wa inu adzandipereka Ine.