Masalimo 135:2 - Buku Lopatulika Inu akuimirira m'nyumba ya Yehova, m'mabwalo a nyumba ya Mulungu wathu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Inu akuimirira m'nyumba ya Yehova, m'mabwalo a nyumba ya Mulungu wathu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa inu amene mumatumikira m'Nyumba ya Chauta, m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu wathu! Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero amene mumatumikira mʼnyumba ya Yehova, mʼmabwalo a nyumba ya Mulungu wathu. |
Ndipo muimirire m'malo opatulika, monga mwa magawidwe a nyumba za makolo za abale anu ana a anthu, akhale nalo onse gawo la nyumba ya makolo ya Alevi.
Nati Alevi, Yesuwa, ndi Kadimiyele, Bani, Hasabineya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya, ndi Petahiya, Imirirani, lemekezani Yehova Mulungu wanu kunthawi za nthawi; ndipo lilemekezeke dzina lanu la ulemerero, lokuzika loposa chilemekezo ndi chiyamiko chonse.
Taonani, lemekezani Yehova, atumiki a Yehova inu nonse, akuimirira m'nyumba ya Yehova usiku.
Mpatseni Yehova ulemerero wa dzina lake; bwerani nacho chopereka, ndipo fikani kumabwalo ake.
zaka zisanu ndi ziwiri, ndipo anali wamasiye wa kufikira zaka zake makumi asanu ndi atatu mphambu zinai, amene sankachoka ku Kachisi, wotumikira Mulungu ndi kusala kudya ndi kupemphera usiku ndi usana.