Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israele, kuyambira kosayamba kufikira kosatha. Ndipo anthu onse anati, Amen! Nalemekeza Yehova.
Masalimo 113:2 - Buku Lopatulika Lodala dzina la Yehova Kuyambira tsopano kufikira kosatha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Lodala dzina la Yehova Kuyambira tsopano kufikira kosatha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yamikani Chauta kuyambira tsopano mpaka muyaya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova atamandidwe, kuyambira tsopano mpaka muyaya. |
Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israele, kuyambira kosayamba kufikira kosatha. Ndipo anthu onse anati, Amen! Nalemekeza Yehova.
Wodala Yehova, Mulungu wa Israele, kuyambira kosayamba kufikira kosatha. Ndi anthu onse anene, Amen. Aleluya.
Wodalitsika Yehova, Mulungu wa Israele, kuchokera nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha. Amen, ndi Amen.
Daniele anayankha, nati, Lilemekezedwe dzina la Mulungu kunthawi za nthawi, pakuti nzeru ndi mphamvu zili zake;
kwa Iye ukhale ulemerero mu Mpingo ndi mwa Khristu Yesu, kufikira mibadwo yonse ya nthawi za nthawi. Amen.
Ndipo cholengedwa chilichonse chili m'mwamba, ndi padziko, ndi pansi padziko, ndi m'nyanja, ndi zonse zili momwemo, ndinazimva zilikunena, Kwa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa zikhale chiyamiko, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi mphamvu, kufikira nthawi za nthawi.