Masalimo 11:3 - Buku Lopatulika Akapasuka maziko, wolungama angachitenji? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Akapasuka maziko, wolungama angachitenji? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ngati maziko aonongeka, nanga wolungama angachite chiyani?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono ngati maziko awonongeka, olungama angachite chiyani?” |
Sadziwa, ndipo sazindikira; amayendayenda mumdima; maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.
Ndipo iwo amene adzakhala a iwe adzamanga malo akale abwinja; udzautsa maziko a mibadwo yambiri; udzatchedwa Wokonza pogumuka, Wakubwezera njira zakukhalamo.
Koma ndithu maziko a Mulungu aimika pokhazikika, ndi kukhala nacho chizindikiro ichi, Ambuye azindikira iwo amene ali ake; ndipo, Adzipatule kwa chosalungama yense wakutchula dzina la Ambuye.