Ndipo Abisalomu anaitana Ahitofele Mgiloni, phungu wa Davide, kumzinda wake ndiwo Gilo, pamene iye analikupereka nsembe. Ndipo chiwembucho chinali cholimba; pakuti anthu anachulukachulukabe kwa Abisalomu.
Masalimo 109:3 - Buku Lopatulika Ndipo anandizinga ndi mau a udani, nalimbana nane kopanda chifukwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anandizinga ndi mau a udani, nalimbana nane kopanda chifukwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ponseponse amandilankhula mau achidani, amandinena popanda chifukwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Andizungulira ndi mawu audani, amandinena popanda chifukwa. |
Ndipo Abisalomu anaitana Ahitofele Mgiloni, phungu wa Davide, kumzinda wake ndiwo Gilo, pamene iye analikupereka nsembe. Ndipo chiwembucho chinali cholimba; pakuti anthu anachulukachulukabe kwa Abisalomu.
Adani anga asandikondwerere ine monyenga; okwiya nane kopanda chifukwa asanditsinzinire.
Pakuti ananditchera ukonde wao m'mbunamo kopanda chifukwa, anakumbira moyo wanga dzenje kopanda chifukwa.
Ondida kopanda chifukwa achuluka koposa tsitsi la pamutu panga; ofuna kunditha, ndiwo adani anga monama, ali ndi mphamvu. Pamenepo andibwezetsa chosafunkha ine.
Efuremu andizinga ndi bodza, ndi nyumba ya Israele ndi chinyengo, ndi Yuda apikisana ndi Mulungu, ndiye Woyera wokhulupirika.
Nati iye, Chifukwa ninji mbuye wanga amalondola mnyamata wake? Pakuti ndachitanji? Kapena m'dzanja langa muli choipa chotani?