Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 109:4 - Buku Lopatulika

4 M'malo mwa chikondi changa andibwezera udani; koma ine, kupemphera ndiko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 M'malo mwa chikondi changa andibwezera udani; koma ine, kupemphera ndiko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 M'malo mwa chikondi changa, iwo amandibwezera zondineneza, ngakhale pamene ndikuŵapempherera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Mʼmalo mwa chikondi changa amandineneza, koma ine ndine munthu wapemphero.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 109:4
14 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu Davide analira kunka kwa Abisalomu, chifukwa anasangalatsidwa pa imfa ya Aminoni.


Ndipo Hanuni anatenga anyamata a Davide, nawameta, nadula malaya ao pakati kufikira m'matako, nawaleka achoke.


Andibwezera choipa m'malo mwa chokoma, inde, asaukitsa moyo wanga.


Pakuti ananditchera ukonde wao m'mbunamo kopanda chifukwa, anakumbira moyo wanga dzenje kopanda chifukwa.


Ndipo iwo akubwezera choipa pa chabwino atsutsana nane, popeza nditsata chabwino.


Wobwezera zabwino zoipa, zoipa sizidzamchokera kwao.


Ndipo podziwa Daniele kuti adatsimikiza cholembedwacho, analowa m'nyumba mwake, m'chipinda mwake, chimene mazenera ake anatseguka oloza ku Yerusalemu; ndipo anagwada maondo ake tsiku limodzi katatu, napemphera, navomereza pamaso pa Mulungu wake monga umo amachitira kale lonse.


Ndipo Yesu ananena, Atate, muwakhululukire iwo, pakuti sadziwa chimene achita. Ndipo anagawana zovala zake, poyesa maere.


Yesu anayankha iwo, Ndakuonetsani inu ntchito zabwino zambiri za kwa Atate; chifukwa cha ntchito yiti ya izo mundiponya miyala?


Ndipo ndidzapereka ndi kuperekedwa konse chifukwa cha miyoyo yanu mokondweratu. Ngati ndikonda inu kochuluka koposa, kodi ndikondedwa kochepa?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa