Masalimo 109:1 - Buku Lopatulika Mulungu wa chilemekezo changa, musakhale chete; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mulungu wa chilemekezo changa, musakhale chete; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Musakhale chete, Inu Mulungu, amene ndimakutamandani, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mulungu amene ndimakutamandani, musakhale chete, |
Kwa Inu, Yehova, ndidzafuulira; thanthwe langa, musandikhalire ngati wosamva; pakuti ngati munditontholera ine, ndidzafanana nao iwo akutsikira kumanda.
Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, ndipo wakhala chipulumutso changa; ameneyo ndiye Mulungu wanga, ndidzamlemekeza; ndiye Mulungu wa kholo langa, ndidzamveketsa.
Ndakhala nthawi yambiri wosalankhula ndakhala chete kudzithungata ndekha; tsopano ndidzafuula ngati mkazi wobala; ndidzapuma modukizadukiza ndi wefuwefu pamodzi.
Mundichiritse ine, Yehova, ndipo ndidzachiritsidwa; mundipulumutse ine, ndipo ndidzapulumutsidwa; pakuti chilemekezo changa ndinu.
Iye ndiye lemekezo lanu, Iye ndiye Mulungu wanu, amene anachita nanu zazikulu ndi zoopsa izi, mudaziona m'maso mwanu.