Fupa langa laumirira pa khungu langa ndi mnofu wanga, ndipo ndapulumuka ndili nazo nkhama za mano anga.
Masalimo 102:6 - Buku Lopatulika Ndikunga vuwo m'chipululu; ndikhala ngati kadzidzi wa kumabwinja. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndikunga vuwo m'chipululu; ndikhala ngati kadzidzi wa kumabwinja. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndili ngati mbalame yakuchipululu, ngati kadzidzi wam'mabwinja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndili ngati kadzidzi wa ku chipululu, monga kadzidzi pakati pa mabwinja. |
Fupa langa laumirira pa khungu langa ndi mnofu wanga, ndipo ndapulumuka ndili nazo nkhama za mano anga.
Ndinalankhulalankhula ngati namzeze, pena chumba; Ndinalira maliro ngati nkhunda; maso anga analephera pogadamira kumwamba. Ambuye ndasautsidwa, mundiperekere chikoli.
Chifukwa cha ichi ndidzachita maliro, ndi kuchema, ndidzayenda wolandidwa ndi wamaliseche; ndidzalira ngati nkhandwe, ndi kubuma ngati nthiwatiwa.
Ndipo zoweta zidzagona pansi pakati pake; nyama zonse za mitundumitundu; ndi vuwo ndi nungu zidzakhala m'mitu ya nsanamira zake; adzaimba mau ao m'mazenera; paziundo padzakhala chipasuko; pakuti anagadamula ntchito yake ya mkungudza.
Ndipo anafuula ndi mau olimba, nanena, Wagwa, wagwa, Babiloni waukulu, nusandulika mokhalamo ziwanda, ndi mosungiramo mizimu yonse yonyansa, ndi mosungiramo mbalame zonse zonyansa ndi zodanidwa.