Zefaniya 2:14 - Buku Lopatulika14 Ndipo zoweta zidzagona pansi pakati pake; nyama zonse za mitundumitundu; ndi vuwo ndi nungu zidzakhala m'mitu ya nsanamira zake; adzaimba mau ao m'mazenera; paziundo padzakhala chipasuko; pakuti anagadamula ntchito yake ya mkungudza. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 Ndipo zoweta zidzagona pansi pakati pake; nyama zonse za mitundumitundu; ndi vuwo ndi nungu zidzakhala m'mitu ya nsanamira zake; adzaimba mau ao m'mazenera; paziundo padzakhala chipasuko; pakuti anagadamula ntchito yake ya mkungudza. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 Choncho zoŵeta zizidzagona kumeneko chimodzimodzinso nyama zonse zakuthengo. Adembo ndi akanungu azidzagona pa makapotolosi ake. Akadzidzi azidzalira pa windo, ndipo makwangwala azidzakhala pa bwalo lake. Mitengo yake yamkungudza adzaisadza. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 Nkhosa ndi ngʼombe zidzagona pansi kumeneko, pamodzi ndi nyama zakuthengo za mtundu uliwonse. Akadzidzi a mʼchipululu ndi akanungu adzakhala pa nsanamira zake. Kulira kwawo kudzamveka mʼmazenera, mʼmakomo mwawo mudzakhala zinyalala zokhazokha, nsanamira za mkungudza zidzakhala poonekera. Onani mutuwo |