Ndiponso Manase anakhetsa mwazi wambiri wosachimwa mpaka anadzaza mu Yerusalemu monsemo, osawerenga kulakwa kwake analakwitsa nako Yuda, ndi kuchita choipa pamaso pa Yehova.
Masalimo 10:8 - Buku Lopatulika Akhala m'molalira midzi; mobisalamo akupha munthu wosachimwa. Ambisira waumphawi nkhope yake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Akhala m'molalira midzi; mobisalamo akupha munthu wosachimwa. Ambisira waumphawi nkhope yake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Amalalira m'midzi, amapha anthu osalakwa m'malo obisalira. Amazondazonda kuti apeze opanda mwai. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye amabisalira anthu pafupi ndi midzi, kuchokera pobisalapo amapha anthu osalakwa, amayangʼanayangʼana mwachinsinsi anthu oti awawononge. |
Ndiponso Manase anakhetsa mwazi wambiri wosachimwa mpaka anadzaza mu Yerusalemu monsemo, osawerenga kulakwa kwake analakwitsa nako Yuda, ndi kuchita choipa pamaso pa Yehova.
Koma maso ako ndi mtima wako sizisamalira kanthu koma kusirira, ndi kukhetsa mwazi wosachimwa, ndi kusautsa, ndi zachiwawa, kuti uzichite.
Munapyoza ndi maluti ake mutu wa ankhondo ake; anadza ngati kamvulumvulu kundimwaza; kukondwerera kwao kunanga kufuna kutha ozunzika mobisika.
Zitapita izi Ambuye anaika ena makumi asanu ndi awiri, nawatuma iwo awiriawiri pamaso pake kumudzi uliwonse, ndi malo ali onse kumene ati afikeko mwini.
Ndipo kunali, katapita kamphindi anayendayenda kumizinda ndi kumidzi, kulalikira ndi kuwauza Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndi pamodzi naye khumi ndi awiriwo,
Ndipo eni ake a ku Sekemu anaika omlalira pamwamba pa mapiri; amene anawawanya onse akudzera njirayi; ndipo anamuuza Abimeleki.
Pamenepo mfumu inati kwa Doegi, Potoloka iwe nuwaphe ansembewo. Ndipo Doegi wa ku Edomu anapotoloka, nagwera ansembewo, napha tsikulo makumi asanu ndi atatu mphambu asanu akuvala efodi wabafuta.
Chifukwa chake yang'anirani, ndi kudziwa ngaka zonse alikubisalamo iye, nimubwere kwa ine ndi mau otsimikizika, pomwepo ndidzamuka nanu; ndipo akakhala m'dzikomo, ndidzampwaira pakati pa mabanja onse a Yuda.