Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 22:18 - Buku Lopatulika

18 Pamenepo mfumu inati kwa Doegi, Potoloka iwe nuwaphe ansembewo. Ndipo Doegi wa ku Edomu anapotoloka, nagwera ansembewo, napha tsikulo makumi asanu ndi atatu mphambu asanu akuvala efodi wabafuta.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Pamenepo mfumu inati kwa Doegi, Potoloka iwe nuwaphe ansembewo. Ndipo Doegi wa ku Edomu anapotoloka, nagwera ansembewo, napha tsikulo makumi asanu ndi atatu mphambu asanu akuvala efodi wabafuta.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Pomwepo mfumu idauza Doegi kuti, “Kaŵaphe ndiwe.” Doegi, Mwedomu uja, adapitadi kukapha ansembewo. Adapha anthu 85 ololedwa kuvala efodi ya thonje lokoma.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Kotero mfumu inalamula Doegi kuti, “Uwaphe ndiwe ansembewa.” Choncho Doegi Mwedomu anapita ndi kuwapha. Tsiku limenelo iye anapha amuna 85 amene amavala efodi wa nsalu yofewa.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 22:18
14 Mawu Ofanana  

Koma anampangira chiwembu, namponya miyala, mwa lamulo la mfumu m'bwalo la nyumba ya Yehova.


Ansembe ao anagwa ndi lupanga; ndipo amasiye ao sanachite maliro.


Ndipo usokere ana a Aroni malaya am'kati, nuwasokere mipango; uwasokerenso akapa akhale aulemerero ndi okoma.


Usabisalire, woipa iwe, pomanga wolungama; usapasule popuma iyepo.


Efuremu azunzika, apsinjika pa mlanduwo; pakuti anafuna mwini wake kutsata lamulolo.


Akondweretsa mfumu ndi zoipa zao, ndi akalonga ndi mabodza ao.


Pakuti asunga malemba a Omuri, ndi ntchito za nyumba ya Ahabu, ndipo mumayenda mu uphungu wao; kuti ndikusandulize bwinja, ndi okhalamo chotsonya; ndipo mudzasenza chitonzo cha anthu anga.


Akalonga ake m'kati mwake ndiwo mikango yobangula; oweruza ake ndi mimbulu ya madzulo, sasiya kanthu ka mawa.


Koma Samuele anatumikira pamaso pa Yehova akali mwana, atamangira m'chuuno ndi efodi wabafuta.


Kodi sindinasankhule iye pakati pa mafuko onse a Israele, akhale wansembe wanga, kuti apereke nsembe paguwa langa, nafukize zonunkhira, navale efodi pamaso panga? Kodi sindinapatse banja la kholo lako zopereka zonse za kumoto za ana a Israele?


Ndipo kudzali kuti yense wakusiyidwa wa m'banja lako adzabwera kwa iye nadzawerama ndi kupempha ndalama ndi chakudya, nadzati, Mundipatsetu ntchito ina ya wansembe, kuti ndikaone kakudya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa