Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 22:19 - Buku Lopatulika

19 Ndipo anakantha Nobu ndiwo mzinda wa ansembe ndi lupanga lakuthwa, anthu aamuna ndi aakazi, ana ndi makanda, ng'ombe ndi abulu, ndi nkhosa, ndi lupanga lakuthwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Ndipo anakantha Nobu ndiwo mudzi wa ansembe ndi lupanga lakuthwa, anthu aamuna ndi aakazi, ana ndi makanda, ng'ombe ndi abulu, ndi nkhosa, ndi lupanga lakuthwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Kunena za Nobu, mzinda wa ansembe uja, Saulo adalamula kuti anthu onse okhalamo aphedwe. Choncho amuna ndi akazi, ana ndi makanda, kudzanso ng'ombe, abulu ndi nkhosa, zonsezo adazipha ankhondo ake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Kunena za Nobi, mzinda wa ansembe, Sauli anapha amuna ndi amayi, ana ndi makanda pamodzi ndi ngʼombe, abulu ndi nkhosa.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 22:19
13 Mawu Ofanana  

pa Anatoti, Nobi, Ananiya,


Lero lomwe adzaima pa Nobu; agwedezera dzanja lake paphiri la mwana wamkazi wa Ziyoni, phiri la Yerusalemu.


Momwemo phokoso lidzaukira anthu ako, ndi malinga ako onse adzapasuka, monga Salimani anapasula Betaribele; tsiku la nkhondo amai anaphwanyika pamodzi ndi ana ake.


nanena kwa Iye, Mulinkumva kodi chimene alikunena awa? Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Inde: simunawerenge kodi, M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza?


Pakuti chiweruziro chilibe chifundo kwa iye amene sanachite chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro.


Koma mzindawo udzaperekedwa kwa Yehova ndi kuonongeka konse, uwu ndi zonse zili m'mwemo; Rahabi yekha wadamayo adzakhala ndi moyo, iye ndi onse ali naye m'nyumba, chifukwa anabisa mithenga tinawatumawo.


Ndipo anapereka kuziononga ndi lupanga lakuthwa zonse za m'mzinda, amuna ndi akazi omwe, ana ndi nkhalamba zomwe, kudza ng'ombe, ndi nkhosa, ndi abulu, ndi lupanga lakuthwa.


Muka tsopano, nukanthe Amaleke, nuononge konsekonse zonse ali nazo, usawalekerere, koma uwaphe mwamuna ndi mkazi, mwana ndi woyamwa, ng'ombe ndi nkhosa, ngamira ndi bulu.


Namtenga wamoyo Agagi, mfumu ya Aamaleke, naononga konsekonse anthu onse ndi lupanga lakuthwa.


Koma Saulo ndi anthu anamsunga wamoyo Agagi, ndi nkhosa zokometsetsa, ndi ng'ombe, ndi zonenepa zina, ndi anaankhosa, ndi zabwino zonse sadafune kuzitha psiti; koma zonse zoipa ndi zonyansa anaziononga konsekonse.


Ndipo Davide anafika ku Nobu kwa Ahimeleki wansembeyo; ndipo Ahimeleki anadza kukomana ndi Davide alikunjenjemera, nanena naye, Muli nokha bwanji, palibe munthu wina nanu?


Pamenepo mfumu anatuma mthenga kukaitana Ahimeleki wansembeyo, mwana wa Ahitubi, ndi banja lonse la atate wake, ansembe a ku Nobu; ndipo iwo onse anafika kwa mfumu.


Pamenepo Doegi wa ku Edomu, anaimirira ndi anyamata a Saulo, nayankha, nati, Ine ndinamuona mwana wa Yeseyo alikufika ku Nobu, kwa Ahimeleki mwana wa Ahitubi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa