Masalimo 10:1 - Buku Lopatulika Muimiranji patali, Yehova? Mubisaliranji m'nyengo za nsautso? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Muimiranji patali, Yehova? Mubisaliranji m'nyengo za nsautso? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chifukwa chiyani mumaima kutali nafe, Inu Chauta? Chifukwa chiyani mumabisala pamene tili pa mavuto? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nʼchifukwa chiyani Yehova mwayima patali? Chifukwa chiyani mukudzibisa nokha pa nthawi ya mavuto? |
Iye akapatsa mpumulo adzamtsutsa ndani? Akabisa nkhope yake adzampenyerera ndani? Chikachitika pa mtundu wa anthu, kapena pa munthu, nchimodzimodzi;
Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine? Mukhaliranji kutali kwa chipulumutso changa, ndi kwa mau a kubuula kwanga?
Musandibisire ine nkhope yanu; musachotse kapolo wanu ndi kukwiya. Inu munakhala thandizo langa; musanditaye, ndipo musandisiye Mulungu wa chipulumutso changa.
Inu, Yehova, munakhazikitsa phiri langa ndi kuyanja kwanu; munabisa nkhope yanu; ndinaopa.
Inu, chiyembekezo cha Israele, Mpulumutsi wake nthawi ya msauko, bwanji mukhala ngati mlendo m'dziko, ngati woyendayenda amene apatuka usiku?
Bwanji mukhala ngati munthu wodabwa, ngati munthu wamphamvu wosatha kupulumutsa? Koma Inu, Yehova, muli pakati pathu, titchedwa ndi dzina lanu; musatisiye.