Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 30:7 - Buku Lopatulika

7 Inu, Yehova, munakhazikitsa phiri langa ndi kuyanja kwanu; munabisa nkhope yanu; ndinaopa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Inu, Yehova, munakhazikitsa phiri langa ndi kuyanja kwanu; munabisa nkhope yanu; ndinaopa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Chifukwa cha kukoma mtima kwanu, Inu Chauta, mudandikhazikitsa ngati phiri lolimba. Koma pamene mudandimana madalitso anu, ine ndidataya mtima.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Inu Yehova, pamene munandikomera mtima, munachititsa phiri langa kuyima chilili; koma pamene munabisa nkhope yanu, ndinataya mtima.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 30:7
16 Mawu Ofanana  

Mwandipatsa moyo, ndi kundikomera mtima, ndi masamalidwe anu anasunga mzimu wanga.


Muimiranji patali, Yehova? Mubisaliranji m'nyengo za nsautso?


chifukwa cha ukali wanu ndi kuzaza kwanu; popeza munandinyamula ndipo munandigwetsa.


Mukabisa nkhope yanu, ziopsedwa; mukalanda mpweya wao, zikufa, ndipo zibwerera kufumbi kwao.


Fulumirani ndiyankheni, Yehova; mzimu wanga ukutha. Musandibisire nkhope yanu; ndingafanane nao akutsikira kudzenje.


Pakuti mkwiyo wake ukhala kanthawi kokha; koma kuyanja kwake moyo wonse. Kulira kuchezera, koma mamawa kuli kufuula kokondwera.


Ndipo anandikweza kunditulutsa m'dzenje la chitayiko, ndi m'thope la pachithaphwi; nandipondetsa pathanthwe, nakhazika mayendedwe anga.


Pakuti sanalande dziko ndi lupanga lao, ndipo mkono wao sunawapulumutse. Koma dzanja lanu lamanja, ndi mkono wanu, ndi kuunika kwa nkhope yanu. Popeza munakondwera nao,


Pakuti Inu, Yehova, mudzadalitsa wolungamayo; mudzamtchinjiriza nacho chivomerezo ngati chikopa.


Popeza Inu ndinu ulemerero wa mphamvu yao; ndipo potivomereza Inu nyanga yathu idzakwezeka.


Taonani, ndinali ndi zowawa zazikulu, chifukwa cha mtendere wanga; Koma Inu mokonda moyo wanga, munaupulumutsa m'dzanja la chivundi, Pakuti mwaponya m'mbuyo mwanu machimo anga onse.


Pamenepo ndidzawapsera mtima tsiku ilo, ndipo ndidzawataya, ndi kuwabisira nkhope yanga, ndipo adzathedwa, ndi zoipa ndi zovuta zambiri zidzawafikira; kotero kuti adzati tsiku lija, Sizitifikira kodi zoipa izi popeza Mulungu wathu sakhala pakati pa ife?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa