Ndipo anakonza nkhunizo, naduladula ng'ombe, naiika pankhuni. Nati, Dzazani madzi mbiya zinai, muwathire pa nsembe yopsereza ndi pankhuni.
Marko 9:2 - Buku Lopatulika Ndipo atapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu anatenga Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, nakwera nao paphiri lalitali padera pa okha; ndipo anasandulika pamaso pao: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo atapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu anatenga Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, nakwera nao pa phiri lalitali padera pa okha; ndipo anasandulika pamaso pao: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Patapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu adatenga Petro ndi Yakobe ndi Yohane, nakwera nawo ku phiri lalitali, kwaokha. Tsono maonekedwe a Yesu adasinthika iwo akuwona. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Patatha masiku asanu ndi limodzi Yesu anatenga Petro, Yakobo ndi Yohane nawatsogolera kupita ku phiri lalitali, kumene anali okhaokha. Kumeneko maonekedwe ake anasinthika pamaso pawo. |
Ndipo anakonza nkhunizo, naduladula ng'ombe, naiika pankhuni. Nati, Dzazani madzi mbiya zinai, muwathire pa nsembe yopsereza ndi pankhuni.
Ndipo Ahabu anakadya, namwa; koma Eliya anakwera pamwamba pa Karimele, nagwadira pansi, naika nkhope yake pakati pa maondo ake.
Pakuti ameneyo adzaphuka pamaso pake ngati mtengo wanthete, ndi ngati muzu womera m'nthaka youma; Iye alibe maonekedwe, pena kukongola; ndipo pamene timuona palibe kukongola kuti timkhumbe.
Ndipo Yesu pakumva, anachokera kumeneko m'ngalawa, kunka kumalo achipululu pa yekha; ndipo makamu, pamene anamva, anamtsata Iye mumtunda kuchokera m'midzi.
Ndipo anatenga pamodzi ndi Iye Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, nayamba kudabwa kwambiri, ndi kusauka mtima ndithu.
Ndipo zitatha izi, anaonekanso Iye m'maonekedwe ena kwa awiri a iwo alikuyenda kupita kumidzi.
Ndipo sanalole munthu yense kutsagana naye, koma Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane mbale wake wa Yakobo.
Ndipo kunali masiku awa, Iye anatuluka nanka kuphiri kukapemphera; nachezera usiku wonse m'kupemphera kwa Mulungu.
Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.
Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.
Nthawi yachitatu iyi ndilinkudza kwa inu. Pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu maneno onse adzakhazikika.
amene adzasanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lake la ulemerero, monga mwa machitidwe amene akhoza kudzigonjetsera nao zinthu zonse.
Ndipo ndinaona, mpando wachifumu waukulu woyera, ndi Iye wakukhalapo, amene dziko ndi m'mwamba zinathawa pamaso pake, ndipo sanapezedwe malo ao.